Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Chithunzi cha a Minos Kokkinakis ali kundende ndi a Mboni ena komanso cha zaka zingapo atatulutsidwa.

JANUARY 7, 2019
GREECE

Nkhondo Yomenyera Ufulu Wolalikira Yomwe Inatenga Zaka 50

Nkhondo Yomenyera Ufulu Wolalikira Yomwe Inatenga Zaka 50

Zaka 80 zapitazo, a Minos Kokkinakis anatumizidwa kuchilumba chakutali chotchedwa Amorgós ku Greece kuti akakhale m’ndende kwa miyezi 13. Khoti lina la ku Greece linanena kuti M’bale Kokkinakis ndi wolakwa chifukwa chophwanya lamulo latsopano lomwe linkaletsa anthu kulalikira kwa ena n’cholinga chowapangitsa kusintha chipembedzo chawo. Izi zinachitika ngakhale kuti a Kokkinakis sanawazenge mlandu. Iwo anali oyamba kumangidwa pa a Mboni za Yehova 19,147 omwe anamangidwa kuyambira mu 1938 mpaka 1992 chifukwa chophwanya lamulolo lomwe linakhazikitsidwa ndi wolamulira wopondereza wina wa ku Greece dzina lake Ioannis Metaxas. Pa zaka 50 zimenezo, abale ndi alongo ambiri ku Greece analalikira uthenga wabwino molimba mtima ngakhale kuti ankamenyedwa, kumangidwa, komanso kutsekeredwa m’ndende.

M’bale Kokkinakis anayamba nkhondo yomenyera ufulu woti azilalikira ali ndi zaka pafupifupi 30 ndipo nkhondoyi inatenga zaka 50. M’baleyu anamangidwapo maulendo opitirira 60 ndipo anakhala zaka zoposa 6 m’ndende ndi m’zilumba zina zomwe zinkagwiritsidwa ntchito ngati ndende. Pa nthawiyi a Kokkinakis ndi a Mboni ena anapirira nkhanza zosaneneka kundendeku. Atafika zaka 77 anamangidwanso komaliza ndipo pa nthawiyi anadandaula kukhoti kuti anamangidwa mopanda chilungamo, koma akhoti anagamula kuti amangidwebe ndipo zimenezi zinachititsa kuti apange apilo kumakhoti ena. Pomalizira pake mlanduwu unaweruzidwanso ndi Khoti Lalikulu Kwambiri ku Greece ndipo linagamulanso kuti ndi olakwa. Chifukwa choti makhoti onse m’dziko la Greece sanapereke ufulu wolambira kwa a Kokkinakis, iwo anakadandaula za nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Mu 1993, a Minos Kokkinakis anapambana pa nkhondo yomenyera ufulu wopembedza ndipo pa nthawiyi anali ndi zaka 84. Aka kanali koyamba kuti Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe ligamule kuti dziko laphwanyira anthu ufulu wopembedza. * Pofika mu 2018, panali patatha zaka 25 kuchokera pamene khotili linapanga chigamulo chosaiwalikachi. Pulofesa wina woona zamalamulo a pakati pa mayiko osiyanasiyana ananena kuti chigamulo cha mlandu wa a Kokkinakis, “ndi chigamulo cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe chomwe anthu ambiri amachigwiritsa ntchito akamanena nkhani zokhudza ufulu wopembedza kapena wochita zinthu zomwe munthu amakhulupirira.”

Maboma ena akamazenga milandu inanso yofanana ndi umenewu angagwiritse ntchito chigamulo chokhudza mlandu wa a Kokkinakis, makamaka panopa pamene maboma amphamvu kwambiri monga Russia akukaniza abale athu kuti asakhale ndi ufulu wopembedza.

Zimene M’bale Kokkinakis anachita posonyeza chikhulupiriro komanso kupirira polalikira, ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa abale ndi alongo omwe akutsutsidwa chifukwa chogwira ntchito yolalikira. Kukhulupirika kwa m’baleyu kwalimbikitsa anthu ambiri mpaka lero.—Aroma 1:8.

^ A Minos Kokkinakis anamwalira mu January 1999.