Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 27, 2018
GREECE

Moto Wolusa Wapha Anthu Komanso Kuwononga Zinthu ku Greece

Moto Wolusa Wapha Anthu Komanso Kuwononga Zinthu ku Greece

Moto wolusa womwe unakula kwambiri chifukwa cha mphepo yamphamvu, unavulaza anthu komanso kuwononga zinthu pafupi ndi mzinda wa Athens ku Greece. Anthu osachepera 76 anafa ndipo enanso 187 anavulala ndi moto wolusawu. Zikuoneka kuti motowu ndi umene wapha anthu ochuluka kwambiri m’dzikoli m’zaka zoposa 10 zapitazi.

Lipoti lochokera ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Greece likusonyeza kuti palibe wa Mboni wina aliyense amene anavulala kapena kufa pa ngoziyi. Komabe, abale ndi alongo athu onse omwe ankakhala m’madera omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi anasamuka, ndipo panopa akukhala m’nyumba za abale a m’mipingo yoyandikana nayo. Komanso nyumba 4 za a Mboni zinawonongeka kwambiri ndipo imodzi inawonongekeratu.

Tikupempherera abale athu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi komanso amene anasonyeza chikondi kwa abale awo powalandira m’nyumba zawo. (Yohane 13:34, 35) Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kuthandiza abale athuwa pa nthawi yovuta imeneyi.