Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Chávez ndi M’bale López akukambirana ndi gulu la nambala 4 la ozimitsa moto mumzinda wa Coatepeque ku Guatemala

DECEMBER 23, 2019
GUATEMALA

Maphunziro Apadera Okhudza Baibulo Akuthandiza Apolisi ndi Ogwira Ntchito Yozimitsa Moto ku Guatemala

Maphunziro Apadera Okhudza Baibulo Akuthandiza Apolisi ndi Ogwira Ntchito Yozimitsa Moto ku Guatemala

Mu May 2019, akuluakulu a boma ku Guatemala anapereka chilolezo kwa abale athu kuti achititse maphunziro apadera okhudza mfundo za m’Baibulo kwa apolisi ndi anthu ogwira ntchito yozimitsa moto. Pofika pano, anthu 450 ogwira ntchito yozimitsa moto ndi apolisi achita nawo maphunzirowa m’mizinda ya Coatepeque, Colomba Costa Cuca, Malacatán, ndi San Rafael Petzal.

Ozimitsa moto akutenga mabuku pakashelefu pambuyo pa maphunziro a Baibulo omwe amachitikira mumzinda wa Colomba Costa Cuca ku Guatemala

A Juan Carlos Rodas omwe ndi mkulu mumpingo ndipo anachititsa nawo maphunzirowa anati: “Kwa zaka zoposa 15, a Mboni za Yehova ku Guatemala akhala akuphunzira Baibulo ndi akaidi m’ndende zitatu. Akuluakulu oyang’anira ndende anaona kuti akaidi omwe tinawaphunzitsa Baibulo anayamba kusintha umunthu wawo. Chifukwa cha zimenezi, akuluakuluwa anatiuza kuti tizikambirananso mfundo za m’Baibulo ndi apolisi komanso ogwira ntchito yozimitsa moto.”

Abale amachititsa maphunzirowa kawiri pa mlungu kwa maminitsi pafupifupi 15 potsatira malangizo omwe anapatsidwa ndi ofesi ya nthambi ya Central America. Iwo amakambirana nkhani zokhudza zimene angachite kuti azigwirizana kwambiri ndi anthu ena, mmene angagwiritsire ntchito ulamuliro moyenera komanso mmene angamagwirire ntchito limodzi mogwirizana. Abalewa amagawira mabuku ogwirizana ndi nkhanizi, amaonetsa mavidiyo a pawebusaiti yathu ndiponso amasonyeza mmene angafufuzire mfundo zofunika pogwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Library.

A Mboni za Yehova amaona kuti ndi mwayi waukulu kukambirana mfundo za m’Baibulo ndi apolisi komanso ogwira ntchito yozimitsa moto. Tikukhulupirira kuti anthuwa apitiriza kupindula ndi nzeru zopindulitsa zochokera m’Baibulo.—2 Timoteyo 3:16.