OCTOBER 15, 2018
HAITI
Kumpoto kwa Dziko la Haiti Kwachitika Chivomezi
Loweruka pa 6 October, 2018, chivomezi champhamvu chinagwedeza chigawo cha kumpoto kwa dziko la Haiti ndipo anthu 17 anafa komanso anthu oposa 300 anavulala.
Malipoti akusonyeza kuti palibe wa Mboni aliyense amene wafa, komabe ofalitsa awiri anavulala. Malipoti oyambirira ochokera kwa oyang’anira madera akusonyeza kuti nyumba 44 komanso Nyumba za Ufumu 4 zinaonongeka. Mumzinda wa Port-de-Paix, abale ndi alongo 50 komanso achibale awo anasamuka m’nyumba zawo kuti apewe ngozi. Abale ndi alongo a m’mipingo yawo akusamalira mabanja amenewa. M’bale wa m’Komiti ya Nthambi ya dziko la Haiti limodzi ndi abale awiri a m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, anapita kumalo omwe kunachitika chivomezichi kuti akaone zomwe zaonongeka komanso kuti akalimbikitse abale ndi alongo. Komiti Yopereka Chithandizo pa Ngozi Zadzidzidzi yakhazikitsidwa kuti iyendetse ntchito yopereka chithandizo chomwe chikufunikira.
Tipitirizabe kuganizira komanso kupempherera abale athu ku Haiti. Tikuyamikira kuti Atate wathu wakumwamba analonjeza kuti adzalimbikitsa atumiki ake okhulupirika mogwirizana ndi kukoma mtima kwake kosatha.—Salimo 119:76.