Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

15 MAY 2017
HAITI

Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudziwa ndi Mphepo Yoopsa Yotchedwa Matthew ku Haiti Yatsala Pang’ono Kutha

Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudziwa ndi Mphepo Yoopsa Yotchedwa Matthew ku Haiti Yatsala Pang’ono Kutha

Komiti yothandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi inakonzanso denga la nyumbayi.

PORT-AU-PRINCE, Haiti—Mphepo yotchedwa Matthew ndi yoopsa kwambiri ndipo inachitikapo kale ku Haiti m’zaka zoposa 50 zapitazo. Mphepoyi inawombanso mwamphamvu m’dziko la Haiti pa 4 October, 2016 ndipo inawononga kwambiri kuposa chivomezi chomwe chinachitika mu 2010 m’dziko lomweli. Lipoti la pa 24 October 2016, lomwe linaulutsidwa pagawo lakuti Malo a Nkhani pawebusaiti yathu ya jw.org, linafotokoza kuti a Mboni za Yehova anathandiza mwamsanga popereka zinthu monga chakudya, mankhwala komanso matenti. Pa 1 January 2017, A Mboni za Yehova anayambanso kupereka thandizo ataonanso kuti pali zinthu zinanso zambiri zomwe zinawonongeka. Ntchitoyi inaphatikizapo kugwiritsa ntchito makomiti atatu othandiza pakachitika ngozi kuti ayang’anire magulu 14 a zomanga ndipo anayamba ntchito yayikulu yokonzanso nyumba zokwana 203 zomwe zinawonongeka. Ntchito yopereka thandizoyi idzatha mu June 2017.

A Daniel Lainé, mneneri wa Mboni za Yehova ku likulu lawo ku Port-au-Prince ananena kuti: “Cholinga cha ntchitoyi n’choti abale ndi alongo athu onse omwe nyumba zawo zinawonongedwa chifukwa cha mphepo yamkuntho zikonzedwenso ndipo asamasowe pokhala.” Koma si zophweka kuti zimenezi zitheke. A Lainé anafotokoza kuti mphepo yamkunthoyi inapangitsa kuti kulumikizana ndi anthu ena kuzikhala kovuta komanso misewu inawonongeka kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti agwire ntchito yopereka thandizoyi movutikira. Pofika pa 20 April, nyumba 96 zinali zitamalizidwa ndipo 30 zinali zikukonzedwabe.

Smith Mathurin, wachiwiri kwa nduna ya Nyumba ya Malamulo ku Paillant ndi ku Petite Rivière de Nippe.

Akuluakulu ena a boma a m’derali anaona zomwe a Mboni anachita pothandiza anzawo. Mwachitsanzo, Smith Mathurin wachiwiri kwa nduna ya Nyumba ya Malamulo m’madera a ku Paillant ndi Petite Rivière de Nippe ananena kuti: “Ngakhale kuti cholinga chachikulu cha a Mboni za Yehova ndi kufalitsa uthenga wabwino, amathandizanso anthu omwe akufunikira thandizo. Ndikuyamikira kwambiri kudzipereka kwa a Mboni za Yehova popereka thandizo kwa anthu amene akhudzidwa ndi mphepo yoopsa kwambiri yotchedwa Matthew. Kunena zoona panafunikadi kuchitapo kanthu ndipo n’zosangalatsa kuti munasiya zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chanu n’kubwera kudzathandiza nawo.”

Munthu akulozera woimira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Haiti denga latsopano lomwe lakonzedwa.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limapereka thandizo pa ntchito yothandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi kuchokera kulikulu lawo ku Warwick, New York. Bungweli limagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo pofuna kuthandiza pa ntchito yophunzitsa anthu Baibulo padziko lonse.

Lankhulani ndi:

Padziko Lonse: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Haiti: Daniel Lainé, +509-2813-1560