Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 11, 2014
HONDURAS

Ku Honduras Kunachitika Ngozi Yoopsa ya Basi

Ku Honduras Kunachitika Ngozi Yoopsa ya Basi

Pa October 31, 2014, mam’mawa, basi yomwe inatenga a Mboni za Yehova 57, omwe anadzipereka kukagwira ntchito yophunzitsa anthu Baibulo ku Las Flores Lempira, inachita ngozi ikuchokera ku San Carlos Choloma. Dalaivala wa basiyi komanso a Mboni 13 anamwalira. Pa anthu a Mboni omwe anamwalirawa panali atsikana awiri azaka 14 ndi mtsikana mmodzi wazaka 8. Anthu 44 omwe anapulumuka anatengedwera kuchipatala kuti akaonedwe ngati avulala. Awiri okha anavulala kwambiri koma panopa anatulutsidwa. A Mboni akutonthoza anthu okhudzidwa ndi ngoziyi komanso akuwathandiza m’njira zosiyanasiyana. Pa November 1, 2014, mwambo woika m’manda anthu 9 omwe anamwalira pangoziyi unachitikira ku Choloma ndipo kunali anthu pafupifupi 3,000.

A José Castillo, omwe amalankhula moimira Mboni za Yehova ku Honduras, ananena kuti: “Tinayamikira kwambiri mmene anthu komanso mabungwe osiyanasiyana anathandizira anthu okhudzidwa ndi ngoziyi.”

Kuchokera M’mayiko Ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Honduras: José Castillo Adriano, tel. +504 9998 0895

Mexico: Gamaliel Camarillo, tel. +52 555 133 3048