APRIL 6, 2016
HUNGARY
Pamalo Osungirako Mbiri Yokhudza Nkhanza za Chipani cha Nazi ku Hungary Panaonetsedwa Chithunzi Cholemekeza a Mboni Amene Anaphedwa
BUDAPEST, Hungary—Pamalo amene amasungirako mbiri yokhudza nkhanza za chipani cha Nazi ku Budapest, panachitika mwambo woonetsa chithunzi cha a Mboni za Yehova 4 omwe anazunzidwa mpaka kuphedwa ndi chipanichi. Mwambowu unachitika pa 11 December, 2015.
Amboni omwe anaphedwawo ndi a Lajos Deli, a Antal Hönisch, a Bertalan Szabó komanso a János Zsondor. Iwo anaphedwa pagulu ndi chipani cha ku Hungary chotchedwa Arrow Cross Nazi Party mu March, 1945 chifukwa chokana ntchito yausilikali. Izi zinachitika m’mizinda ya Körmend ndi Sárvár panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Pachithunzi chomwe chinaonetsedwa pamwambowu, pali mayina a anthuwa komanso mawu a m’Baibulo a palemba la Machitidwe 5:29 akuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”
Potsegulira mwambowu, a Dr. Csaba Latorcai, omwe ndi wachiwiri kwa mlembi woyang’ana nkhani zomwe zikukhudza kwambiri anthu, ananena kuti: “Cholinga cha chithunzichi ndi kukumbukira anyamata 4 a Mboni za Yehova, . . . iwo ankamvera lamulo lakuti ‘usaphe’ ndipo ankatsatira zimene chikumbumtima chawo chinkawauza kuti sayenera kumenyana ndi okhulupirira anzawo komanso munthu wina aliyense.”
Munthu winanso amene anayankhula pamwambowu ndi a Dr. Szabolcs Szita, omwe ndi mkulu woyang’anira pamalowa. Iwo ananena kuti: “Kuonetsedwa kwa chithunzichi ndi nkhani yosangalatsa kwambiri chifukwa kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akuiwalidwa monga anthu amene anazunzika panthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi. Anyamata 4 amene anaphedwawa anali ndi chikhulupiriro cholimba chimene chinawathandiza kuti apitirizebe kukhala okhulupirika mpaka imfa. Iwo ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa tonsefe masiku ano.”
Yankhulani ndi:
International: David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Hungary: András Simon, tel. +36 1 401 1118