1 NOVEMBER 2023
INDIA
A Mboni Akutonthozana Pambuyo pa Mabomba Omwe Anaphulitsidwa Pamsonkhano ku India
Mogwirizana ndi lipoti laposachedwapa lomwe linatulutsidwa pa jw.org, mabomba angapo anaphulitsidwa pamsonkhano womwe unachitika Lamlungu pa 29 October 2023 ku Kerala, m’dziko la India. N’zomvetsa chisoni kuti kuwonjezera pa alongo awiri omwe anaphedwa patsikuli, mtsikana wazaka 12 nayenso wamwalira chifukwa chovulala pachiwembuchi. Abale ndi alongo 55 anavulala ndipo ena anapsa modetsa nkhawa.
Panopa, alongo atatu ndi m’bale mmodzi adakali m’chipatala ndipo sali bwino kwenikweni. Apolisi atsimikizira kuti mabomba osachepera atatu anaphulitsidwa pamene pemphero loyamba linkaperekedwa cha m’ma 9:40 m’mawa. Munthu yemwe akuganiziridwa kuti anachita chiwembu choopsachi ali m’manja mwa apolisi ndipo apolisi ali mkati mofufuza nkhaniyi.
Tikuthokoza kwambiri anthu othandiza pangozi za mwadzidzidzi omwe anafika pamalowa mwachangu ndiponso ogwira ntchito kuchipatala omwe akuthandiza anthu ovulala.
Anthu omwe anali pamsonkhanowu anachita chidwi kwambiri kuona chikondi chimene Akhristu anzawo anasonyezana. Mlongo wina yemwe anapezeka pamsonkhanowu ananena kuti: “Nthawi yomweyo ndinayamba kupemphera kwa Yehova. Olandira alendo limodzi ndi abale ena anatisamalira bwino kwambiri ndipo anachita zinthu mwamsanga kuti titetezeke. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amatikonda komanso amatiganizira aliyense payekha.”
Abale ochokera ku ofesi ya nthambi ya India, oyang’anira madera komanso akulu akupitiriza kulimbikitsa mwauzimu komanso kuthandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi chiwembuchi. Mkulu wina wochokera ku ofesi ya nthambi anapita ku Kerala kukatonthoza abale ndi alongowa, ndipo anati: “Ngakhale kuti abalewa akumva ululu komanso ali ndi mantha kwambiri, ndalimbikitsidwa kwambiri kuona kuti akuonabe zinthu moyenera. Ambiri mwa iwo ndinalankhulana nawo ndipo chikhulupiriro changa mwa Yehova chalimba kwambiri kuona kuti akupitiriza kudalira Yehova.”
A Mboni za Yehova tonse padziko lonse, tikupempherera achibale a anthu omwe anamwalira ndi ena onse amene anakhudzidwa ndi chiwembu choopsa chimene chinachitika ku India. Zimene Baibulo limatilonjeza kuti m’tsogolomu simudzakhalanso zachiwawa, kuvutika komanso imfa, zimatitonthoza komanso kutithandiza kukhala ndi mtendere wamumtima. Ndife otsimikiza kuti sitisiya kukhulupirira komanso kudalira Yehova.—Salimo 56:3.