Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 31, 2019
INDIA

A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Chitelugu ku India

A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Chitelugu ku India

Pa 25 October, 2019, M’bale Ashok Patel yemwe amatumikira m’Komiti ya Nthambi ya India anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Chitelugu pamsonkhano wachigawo womwe unachitikira ku Hyderabad International Convention Centre mumzinda wa Hyderabad ku India.

Anthu pafupifupi 91.9 miliyoni amalankhula Chitelugu chomwe ndi chinenero chachitatu pa zinenero zomwe zimalankhulidwa ndi anthu ambiri ku India. Zina ndi Chihindi komanso Chibengali. Panopa kuli ofalitsa pafupifupi 6,000 omwe amatumikira m’gawo lolankhula Chitelugu koma chiwerengero chonse cha anthu omwe anapezeka pamsonkhanowu chinali 8,868. Zimenezi zikusonyeza kuti pali anthu ambiri olankhula Chitelugu omwe akufuna kuphunzira choonadi chifukwa chaka chino madera awiri atsopano awonjezeka kale.

M’bale wina yemwe anagwira nawo ntchito yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano la Chitelugu yomwe inatenga zaka 5, ananena kuti achinyamata amavutika kumva zomwe amawerenga m’Mabaibulo ena a Chitelugu chifukwa muli mawu achikalekale komanso ovuta. Iye anati, “Achinyamata akamawerenga Baibuloli, zizikhala ngati Yehova akulankhula nawo mwachindunji pogwiritsa ntchito mawu omveka bwino ndiponso amakono ndipo sazivutikanso kumva.” Womasulira wina anawonjezera kuti, “Tikamawerenga lemba linalake mu utumiki, nthawi yomweyo anthu azimva zimene likunena.”

Kuwonjezera pamenepa, Baibulo la Dziko Latsopano lithandiza anthu olankhula Chitelugu kudziwa dzina la Mulungu Wamphamvuyonse popeza kuti m’Mabaibulo ambiri a Chitelugu anachotsamo dzina la Mulungu lakuti Yehova. Baibuloli lithandizanso anthu kuti akamaliwerenga azimvetsa zimene mawu monga akuti moyo ndi mzimu, ankatanthauza m’chinenero choyambirira chomwe Baibulo linalembedwa. Zimenezi n’zosiyana ndi Mabaibulo ena a Chitelugu omwe anamasulira mawuwa mogwirizana ndi zikhulupiriro za chipembedzo cha Chihindu.

Wofalitsa wina anati: “Ndikuona kuti Baibulo la Chitelugu lithandiza anthu amene aziliwerenga kuzindikira kuti Yehova amawakonda kwambiri!” N’zoonekeratu kuti kukhala ndi Baibulo la Dziko Latsopano m’Chitelugu kuthandiza anthu omwe aziliwerenga ‘kulawa ndi kuona kuti Yehova ndi wabwino.’​—Salimo 34:8.