Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 28, 2021
INDIA

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chitamiwu Linatulutsidwa Mzilembo za Chiromani ku India

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chitamiwu Linatulutsidwa Mzilembo za Chiromani ku India

Pa 27 June 2021, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la chilankhulo cha Chitamiwu linatulutsidwa mzilembo za Chiromani. Abale ndi alongo olankhula Chitamiwu omwe akukhala mmaiko okwana 16, anaonera pulogalamu ya kutulutsidwa kwa Baibuloluli kudzera pa intaneti.

Zokhudza Pulojekitiyi

  • Chilankhulo cha Chitamiwu chimalankhulidwa ndi anthu pafupifupi 85 miliyoni padziko lonse

  • Ofalitsa oposa 20,500 akutumikira mmipingo 334 ya Chitamiwu komanso magulu 32

  • Omasulira okwanira 5 anagwira ntchito miyezi 6 kuti amalize pulojeketiyi

Baibulo la Dziko Latsopano la zilembo za Chitamiwu linatulutsidwa mu September 2016. Kutulutsidwa kwa Baibuloli anali madalitso aakulu kwambiri kwa anthu olankhula Chitamiwu padziko lonse. Koma anthu ena olankhula chilankhulochi ankavutika kuwerenga zilembo za Chitamiwu ndipo ankafuna Baibulo la zilembo za Chiromani.

Munthu wina yemwe amagwira ntchito yomasulira anafotokoza kuti ankavutika akamaphunzira Baibulo payekha. Iye anati: “Ndinkavutika kuwerenga zilembo za Chitamiwu moti ndinkagwiritsa ntchito Baibulo la Chingelezi. Baibulo latsopanoli lindithandiza kwambiri.”

Tili ndi chikhulupiriro chonse kuti Baibulo limeneli lithandiza abale ndi alongo ambiri kuwerenga Mawu a Mulungu ndi ‘kuwasinkhasinkha’ komanso kuti azisangalala pa moyo wawo ndiponso kuthandiza ena mu utumiki.​—Yoswa 1:8.