AUGUST 16, 2019
INDIA
Madzi Osefukira Awononga Kumadzulo kwa India
Malinga ndi malipoti a ofalitsa nkhani, madzi osefukira ku India apha anthu osachepera 169 m’madera a Gujarat, Maharashtra, Karnataka, ndi Kerala, omwe ali kumadzulo kwa dzikoli.
Ofesi ya nthambi ku India yanena kuti palibe m’bale kapena mlongo amene anafa kapena kuvulala ndi madzi osefukirawo. Izi ndi zimene ofesiyi yanena.
Ku Gujarat: Mumzinda wa Vadodara, ofalitsa 145 anakhudzidwa ndi madzi osefukira. Ofesi ya omasulira mabuku ya Gujarati, yomwe ili mumzinda wa Vadodara, sinawonongeke.
Ku Maharashtra: Mumzinda wa Mumbai, nyumba za mabanja 6 zinakhudzidwa. Mumzinda wa Sangli, womwe uli pamtunda wa makilomita 378 kum’mwera chakum’mawa kwa Mumbai, ofalitsa 25 anathawa m’nyumba zawo. Abale a mumzinda wapafupi ndi amene anawapatsa malo okhala ongoyembekezera.
Ku Karnataka: Mabanja 6 anathawa m’nyumba zawo chifukwa cha madzi osefukirawo. Derali ndi kumene kuli ofesi ya nthambi, koma ofesiyi sinakhudzidwe ndi mvula yamphamvu kapena madzi osefukira.
Ku Kerala: Mabanja 100 anasamukira kumalo okwera ndipo akukhala ndi a Mboni ena mongoyembekezera. Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi ikufufuza mmene zinthu zilili.
Ofesi ya nthambi ikutsogolera pa ntchito yopereka chithandizo m’madera omwe akhudzidwa. Oyang’anira madera komanso abale a m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga akhala akugwira ntchito mwakhama kuona mmene zinthu zilili komanso kuthandiza abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa. Ntchitoyi ikuphatikizapo kuwapatsa zinthu zofunika monga madzi akumwa, ndiponso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.
Tikupemphera kuti Yehova apitirize kuthandiza abale athu omwe akhudzidwa ndi madzi osefukirawa. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene ngozi zadzidzidzi zidzalowedwa m’malo ndi “mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11.