Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 18, 2020
INDIA

Ogwira Ntchito Yomasulira ku India Apeza Njira Zina pa Nthawi ya Mliri

Ogwira Ntchito Yomasulira ku India Apeza Njira Zina pa Nthawi ya Mliri

Abale ndi alongo omwe amagwira ntchito yomasulira m’maofesi 11 omasulira mabuku ku India, akumana ndi zovuta zina chifukwa cha mliri wa COVID-19. Ku maofesiwa amamasulira mabuku ndi zinthu zina m’zinenero 36. Komabe pofuna kuthana ndi mavuto omwe akukumana nawo, omasulirawa akudalira Yehova ndipo apeza njira zina kuti apitirizebe kugwira ntchito yawo.

Pomasulira mabuku athu, omasulira amafunika kugwirira ntchito pamodzi. Koma mliri wa COVID-19 unachititsa kuti dziko la India likhazikitse malamulo oletsa anthu kuyenda komanso kukhala moyandikana. Zimenezi zinakhudza abale ndi alongo omwe amagwira ntchito yomasulira moti sangakumanenso malo amodzi. Komanso zinakhudza abale ndi alongo omwe amajambula mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera kumaofesi omasulirawa.

Abale ndi alongowa anayamba kulumikizana kudzera pa vidiyokomfelensi komanso kujambula zinthu m’malo ena. Kuchita zimenezi kwathandiza kuti omasulira azithandizidwanso ndi abale ndi alongo a m’mayiko ena monga ku Bangladesh ndi ku United States.

Abalewa akugwiritsanso ntchito njira zatsopano pomasulira mavidiyo m’chinenero chamanja ndipo akuyesetsa kutsatira malangizo oti azikhala motalikirana. Ena akonza masitudiyo ojambulira zinthu m’zipinda zawo ndipo akugwiritsa ntchito zinthu zina m’malo mwa zipangizo zapadera. Mwachitsanzo, akumagwiritsa ntchito mafoni awo a m’manja m’malo mwa makamera apamwamba ndipo akumawakhazika pa mabolodi m’malo moika pa masitandi a kamera.

Kuwonjezera pa zonsezi, omasulirawa akudalira Yehova kuti awathandize kukhalabe achimwemwe komanso akhama pamene akugwira ntchito yawo pa nthawi ya mliriwu. Onani zimene ena mwa omasulirawa ananena.

M’bale Jose Francis wa ku Kolkata anati: “Anthu akakhala pa mavuto, akhoza kumangoganizira za mavuto koma Yehova amapeza njira zothana ndi mavutowo.”

Mlongo Bindu Rani Chandan wa ku Bangalore anati: “Popeza ndikudziwa kuti Yehova akundigwiritsa ntchito pa nthawi yovuta kwambiri imeneyi, ndikumakhala wachimwemwe ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto.”

Mlongo Rubina Patel wa ku Vadodara anafotokoza mmene akumvera mumtima mwake kuti: “Palibe chinthu chimene chingalepheretse Yehova ndi gulu lake. Ngakhale matenda a colonavairasi sangalepheretse.”

Timawanyadira kwambiri abale ndi alongo athu omwe akugwira ntchito yomasulira mwakhama. Sitikukayikira kuti mphamvu ya mzimu woyera ndi yomwe ikuwathandiza kuti azikwanitsa kuchita zimenezi komanso mzimu wa Yehova ukuthandiza kukwaniritsa ulosi wa Yesu wakuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.”—Mateyu 24:14.”