Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 11, 2014
INDIA

Zimene Khoti Lalikulu la ku India Linagamula Zaka 30 Zapitazo Zathandiza Kuti Anthu Akhale ndi Ufulu Wolankhula

Zimene Khoti Lalikulu la ku India Linagamula Zaka 30 Zapitazo Zathandiza Kuti Anthu Akhale ndi Ufulu Wolankhula

Pa July 8, 1985, ana atatu ochokera m’tauni ya Kerala, yomwe ili kum’mwera chakumadzulo kwa dziko la India, anapita ku sukulu monga mwa nthawi zonse. Koma pa tsiku limeneli mphunzitsi wamkulu wa pa sukulupo analamula kuti ana a sukulu akaimbe nyimbo ya fuko m’kalasi. Mwana aliyense ankafunika kuimirira ndiponso kuimba nawo nyimboyo. Ana atatu aja, Bijoe wa zaka 15 limodzi ndi azichemwali ake awiri omwe mayina awo ndi Binu Mol wa zaka 13 ndi Bindu wa zaka 10, sanachite zimene mphunzitsiyo analamula. Popeza kuti anawa anali a Mboni za Yehova, chikumbumtima chawo sichinawalole kuti aimbe nawo nyimboyi. Iwo ankakhulupirira kuti kuchita zimenezi kunali ngati kulambira mafano komanso kukanasonyeza kuti ndi osakhulupirika kwa Yehova.

Zimenezi zitachitika, bambo wa anawo a V. J. Emmanuel, anakambirana  ndi mphunzitsi wamkulu komanso aziphunzitsi ena akuluakulu n’kugwirizana kuti anawo asamaimbe nawo nyimbo ya fuko koma akhoza kumaphunzirabe pasukulupo koma saziimba nawo nyimbo ya fuko. Koma munthu wina wogwira ntchito pa sukulupo anamva zimene ankakambiranazo ndipo anakauza akuluakulu a boma za nkhaniyi. Kenako nkhaniyo inafika kwa MP wa deralo amene anapititsa nkhaniyi ku nyumba ya malamulo chifukwa anaona kuti anawo anasonyeza kuti sakonda dziko lawo. Atangomaliza kukambirana nkhaniyi, mkulu woyendera sukulu analamula mphunzitsi wamkulu uja kuti achotse sukulu ana atatu aja, koma ngati sakufuna kuchotsedwa, anawo avomereze kuti aziimba nyimbo ya fukoyo. Bambo a ana aja anayesetsa kukambirana ndi akuluakulu a sukuluyo kuti asawachotse sukulu koma anawachotsabe. Kenako bambowo analembera kalata Khoti Lalikulu la m’dera la Kerala yopempha kuti khotili ligamule kuti anawa asachotsedwe sukulu. Khotilo linakana zimene bambo Emmanuel anapempha ndipo anachita apilo ku Khoti Lalikulu la m’dziko la India.

Khoti Lalikulu Linagamula Mogwirizana ndi Malamulo Onena za Ufulu wa Anthu

Pa August 11, 1986, Khoti Lalikulu la m’dziko la India linagamula mlanduwu mosiyana ndi zimene Khoti Lalikulu la ku Kerala linagamula. Khotili linanena kuti kuchotsa ana sukulu chifukwa chakuti “chikumbumtima chawo sichikuwalola kuchita zinthu zosemphana ndi chikhulupiriro cha chipembedzo chawo,” ndi kuphwanya malamulo a dziko la India. Woweruza wa khotili, dzina lake O. Chinnappa Reddy, ananena kuti: “Palibe lamulo . . . lomwe limakakamiza aliyense kuimba nyimbo.” Khotili linanenanso kuti ngati munthu ali ndi ufulu wolankhula komanso wofotokoza maganizo ake ndiye kuti alinso ndi ufulu wokhala chete. Linanenanso kuti kuimirira pa nthawi yoimba nyimbo ya fuko ndi ulemu wokwanira. Khotili linagamula kuti akuluakulu a pa sukuluyo alole kuti anawo adzayambirenso sukulu.

Woweruza uja ananenanso kuti: “[A Mboni za Yehova] kaya ndi a ku India, ku Britain, ku America komanso mayiko ena onse padziko lapansi saimba nyimbo ya fuko. . . . Iwo saimba nyimbo ya fuko chifukwa zimene amakhulupirira m’chipembedzo chawo siziwalola kuchita nawo miyambo yokhudza kupemphera kupatulapo kupemphera kwa Mulungu wawo, yemwe ndi Yehova.”

Mlanduwu Unathandiza Kuti Pakhale Ufulu Wachipembedzo

Mlandu wa anawa ndi wofunika kwambiri m’dziko la India chifukwa unathandiza anthu kudziwa kuti palibe lamulo limene limakakamiza munthu kuchita zinthu zomwe chikumbumtima chake sichikumulola ngati zikusemphana ndi zimene amakhulupirira m’chipembedzo chake. Khotilo linavomereza kuti boma likhoza kulanda ufulu wa anthu ngati likuona kuti ufuluwo ukhoza kusokoneza chitetezo cha anthu, kulimbikitsa khalidwe loipa kapena ngati moyo wa anthu uli pangozi. Koma pochita zimenezi bomalo siliyenera kukhwimitsa zinthu komanso kukhazikitsa malamulo osamveka bwinobwino. Khotilo linagamula kuti: “Kukakamiza mwana wa sukulu aliyense kuti aziimba nyimbo ya fuko ngakhale chikumbumtima chake sichikumulola . . . ndi kuphwanya ufulu wa munthu malinga ndi lamulo lopezeka mu Gawo 19(1)(a) ndi mu Gawo 25(1) [m’malamulo a dziko la India].”

Chigamulo chimene khotili linapereka chinathandizanso kuti zipembedzo zing’onozing’ono zikhale ndi ufulu wochita zinthu. Khotilo linanenanso kuti: “Ngati tikunena kuti boma lathu limayendera ulamuliro wa demokalase ndiye kuti dziko lathu liyenera kukhazikitsa malamulo omwe angapereke mwayi kwa anthu omwe ali m’zipembedzo zing’onozing’ono woti azitsatira mfundo zimene amakhulupirira.” Woweruza uja ananenanso kuti: “Pogamula nkhani ngati zimenezi sitiyenera kungotsatira maganizo athu. Ngati zimene munthuyo amakhulupirira zili zomveka komanso ngati chikumbumtima chake sichikumulola kuchita zimenezo ndiye kuti lamulo lopezeka mu Gawo 25 [m’malamulo athu] likhoza kugwira ntchito poteteza ufulu wa munthuyo.”

Woweruza milandu dzina lake O. Chinnappa Reddy ananena kuti: “Chikhalidwe chathu chimatiphunzitsa kulolerana, mfundo zimene timayendera zimatilimbikitsa kulolerana komanso malamulo a m’dziko lathu amatilimbikitsa kulolerana, choncho tiyeni tisasiye kulolerana.”

Mmene Chigamulochi Chikuthandizira Anthu

Nkhani ya anawa inafalitsidwa kwambiri m’manyuzipepala a m’dziko la India komanso anaikambirana m’nyumba ya malamulo ya m’dzikoli. Panopo anthu amene akuphunzira za malamulo amaphunzira za nkhaniyi komanso chigamulo chimene khoti lija linapereka. Anthu amene amalemba nkhani zokhudza malamulo komanso manyuzipepala amanena kuti nkhaniyi ndi yodziwika kwambiri komanso kuti pakakhala nkhani yokhudza kulolerana azitengera chigamulo chimene chinaperekedwa pa nkhani imeneyi. Chigamulocho chikuthandizanso kuti zipembedzo zambiri za m’dzikoli zikhale ndi ufulu wochita zinthu. Chikuthandizanso kuti anthu azilankhula zinthu momasuka akaona kuti ufulu wawo sukulemekezedwa.

Mlanduwu Wateteza Ufulu wa Anthu Onse ku India

Banja la a Emmanuel panopo (mzere wakumbuyo kuyambira kumanzere kupita kumanja) Binu, Bijoe ndi Bindu; (mnzere wakutsogolo) Bambo V. J. Emmanuel ndi a Lillykutty

Pa nthawi imene nkhaniyi inkachitika, banja la a Emmanuel linkanyozedwa, kuopsezedwa ndi akuluakulu a boma komanso kuuzidwa kuti aphedwa. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto amenewa, sadandaula chifukwa anakhalabe okhulupirika pa zimene amakhulupirira m’chipembedzo chawo. Mtsikana mmodzi wa m’banjali dzina lake Bindu, amene panopo anakwatiwa ndipo ali ndi mwana, ananena kuti: “Nditakumana ndi loya wina ndinadabwa kwambiri atandiuza kuti anaphunzira nkhani yathu pamene anali kusukulu yophunzitsa za malamulo. Anathokoza kwambiri zimene a Mboni za Yehova anachita pomenyera nkhondo ufulu wa anthu.”

Bambo wa ana aja ananena kuti: “Chaposachedwapa ndinakumana ndi woweruza milandu dzina lake K. T. Thomas, yemwe panopa anapuma pa ntchito. Atadziwa kuti ndine bambo wa ana atatu amene ankaimbidwa milandu yokhudza kuimba nyimbo ya fuko, anandithokoza kwambiri ndipo anandiuza kuti akakhala ndi mwayi wolankhula pamsonkhano wa maloya, salephera kunena za nkhani yathuyi chifukwa amaona kuti inathandiza kwambiri pa nkhani ya ufulu wa anthu.”

Tsopano papita zaka pafupifupi 30 kuchokera pamene chigamulo chija chinaperekedwa koma nkhaniyi ndi imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zikuthandizabe kuti anthu azikhala ndi ufulu wa kulankhula m’dziko la India. A Mboni za Yehova amasangalala kudziwa kuti anathandiza nawo pa nkhani yoti anthu onse a ku India akhale ndi ufulu womwe ndi wovomerezeka m’malamulo a m’dzikoli.