Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 28, 2018
INDIA

Mphepo Yamkuntho ya Gaja Yawononga ku India

Mphepo Yamkuntho ya Gaja Yawononga ku India

Pa 16 November, 2018, mphepo yamkuntho ya Gaja inawononga kwambiri m’dera la Tamil Nadu lomwe lili kum’mwera kwa dziko la India. Anthu pafupifupi 46 anafa, enanso pafupifupi 250,000 anathawa m’nyumba zawo ndipo nyumba zoposa 85,000 zinawonongeka.

Nyumba ya mmodzi wa abale athu ku Mannargudi, m’dera la Tamil Nadu, imene inawonongeka ndi mtengo womwe unagwa.

Ofesi ya nthambi ya ku India inanena kuti palibe m’bale kapena mlongo yemwe anavulala kapena kuphedwa ndi mphepoyi. Komabe, nyumba 38 za abale athu komanso Nyumba za Ufumu ziwiri zinawonongeka. Ofesi ya nthambi inakhazikitsa Komiti Yopereka Chithandizo Pangozi Zadzidzidzi kuti iyendetse ntchito yothandiza anthu omwe anakhudzidwa, yomwe ikuphatikizapo kugawa chakudya ndi madzi kwa ofalitsa omwe anakhudzidwa.

Tikupempherera abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi mphepo yamkuntho ya Gaja kuti Yehova awatonthoze pogwiritsa ntchito akulu omwe ndi achikondi.—1 Petulo 5:2.