AUGUST 17, 2018
INDIA
Mvula Yamphamvu Yapha Anthu Kum’mwera Chakumadzulo kwa India
Mvula yamphamvu kwambiri yomwe inagwa ku Kerala m’dziko la India, inachititsa kuti nthaka igumuke m’malo 25, komanso kupha anthu osachepera 75. Malinga ndi zimene a Dipatimenti Yoona Zanyengo ku India ananena, mphepo yomwe ikuwomba kuchokera kum’mwera chakumadzulo yachititsa kuti m’dera la Kerala mugwe mvula yamphamvu kwambiri yomwe siinagwepo m’mbuyomu.
Tili ndi chisoni chifukwa cha lipoti limene talandira kuchokera ku ofesi ya nthambi ya ku India. Lipotilo linanena kuti banja lina la Mboni la zaka za m’ma 60, komanso munthu wina yemwe ankaphunzira Baibulo, anafa chifukwa cha kugumuka kwa nthaka. Anthu enanso awiri omwe ankaphunzira Baibulo anavulala kwambiri ndipo panopa ali m’chipatala koma akupezako bwino. Kuonjezera pamenepo, m’bale wina wazaka 17 anamira pamene ankayesa kupulumutsa munthu wina woyandikana naye nyumba.
Ofesi ya nthambi inakhazikitsa Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi kuti ifufuze kuchuluka kwa zinthu zomwe zinaonongeka, komanso kuti iyendetse ntchito yothandiza anthu okhudzidwa. Nyumba za Ufumu zina zikugwiritsidwa ntchito ngati malo amene ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ikuchitikira. Malipoti omwe anaperekedwa ngoziyi itangochitika kumene, akusonyeza kuti nyumba zosachepera 46 za abale zinawonongeka pang’ono kapena zinawonongekeratu. Mabanja 85 (ofalitsa 475) akukhala mongoyembekezera m’nyumba za abale ena kapena za achibale awo. Ofesi ya nthambi inanena kuti m’Nyumba za Ufumu zina munalowa madzi osefukirawo. Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi ili tcheru chifukwa zikuoneka kuti mvula yamphamvuyi ipitirizabe kugwa masiku akubwerawa.
Abale oimira ofesi ya nthambi, woyang’anira dera, komanso akulu m’mipingo, anakayendera abale ndi alongo okhudzidwa kuti akawatonthoze komanso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Malemba.
Tikuganizira komanso kupempherera anthu onse omwe akhudzidwa ndi mvula yowonongayi. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene ngozi ngati zimenezi komanso kupweteka komwe kumabwera chifukwa cha ngozizi, sizidzakhalakonso.—Chivumbulutso 21:3, 4.