Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku India
A Mboni za Yehova anayamba kupezeka ku India kuyambira mu 1905. Iwo anakhazikitsa ofesi yawo ku Bombay (komwe panopa kumatchedwa kuti Mumbai) mu 1926, ndipo analembetsa kukhala chipembedzo chovomerezeka ndi boma mu 1978. A Mboni amapindula ndi malamulo oyendetsera dziko la India chifukwa malamulowo amapatsa anthu ufulu wolambira komanso wouza ena zimene amakhulupirira. Chigamulo chokomera a Mboni chomwe chinaperekedwa ndi Khoti Lalikulu Kwambiri ku India pa mlandu wa Bijoe Emmanuel v. State of Kerala, chinathandiza kwambiri nzika zonse za dziko la India kuti zizisangalala ndi ufulu wopembedza. Tinganene kuti a Mboni za Yehova ku India ali ndi ufulu wopembedza. Komabe, m’zigawo zina za dzikoli gulu la anthu achiwawa lakhala likuwaukira ndiponso kuchita zinthu zina zosonyeza kudana ndi chipembedzo chawo.
Mu 1977, Khoti Lalikulu Kwambiri linasiyanitsa pakati pa kuuza ena za chipembedzo chako ndi kuwakopa kuti alowe m’chipembedzocho. Khotili linanena kuti palibe amene ali ndi ufulu wokopa anthu ena kuti alowe m’chipembedzo chake ndipo linavomereza kuti malamulo oletsa anthu kuchita zimenezi amene zigawo zina za dzikolo zinakhazikitsa ndi ovomerezeka ndithu. Ndiye anthu achipongwe amene amaukira a Mboni nthawi zambiri amagwiritsa ntchito zimene khotili linanena ponamiza apolisi kuti a Mboniwo anawapeza akukopa anthu kuti alowe m’chipembedzo chawo. M’zigawo zomwe sagwiritsa ntchito lamuloli, anthu otsutsawa amanena kuti a Mboni amanyoza Mulungu. Iwo amanena zimenezi pogwiritsa ntchito molakwika lamulo lakalekale n’cholinga chofuna kuletsa ntchito yolalikira yomwe a Mboni amagwira. Zimenezi zachititsa kuti a Mboni azunzidwe ndi magulu a anthu ochita zankhanza maulendo oposa 150 kuyambira m’chaka cha 2002. Nawonso akuluakulu a m’madera omwe a Mboni amachitiridwa zankhanza ndi amene amachititsa kuti nkhanzazi zizipitirira chifukwa sateteza a Mboniwo mokwanira ndiponso saimba milandu magulu a anthu ochita zachiwawa.
A Mboni za Yehova ku India akupitiriza kukadandaula kuboma komanso ku makhoti pofuna kumenyera ufulu wawo wopembedza. Iwo akuyembekezera kuti akuluakulu a m’maderawa komanso anthu onse adzamvera zimene Khoti Lalikulu Kwambiri ku India linanena pa mlandu wa a Bijoe kuti: “Chikhalidwe chathu chimatiphunzitsa kulolerana, mfundo zimene timayendera zimatilimbikitsa kulolerana komanso malamulo a m’dziko lathu amatilimbikitsa kulolerana, choncho tiyeni tisasiye kulolerana.” A Mboni za Yehova akukhulupirira kuti khama lawo lithandiza kuti magulu achiwawa asiye kuwachitira nkhanza komanso kuti pakhale kulolerana pa nkhani zachipembedzo.