DECEMBER 4, 2020
INDONESIA
Baibulo la Dziko Latsopano Lathunthu Latulutsidwa M’zinenero 4 za ku Indonesia
Pa 28 November 2020, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lathunthu linatulutsidwa pazipangizo zamakono komanso losindikizidwa m’zinenero 4 za ku Indonesia ndipo zinenerozi ndi: Chibataki ku Karo, Chibataki ku Toba, Chijavanesi ndi Chiniyasi. M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anatulutsa Mabaibulowa pa nkhani yapadera yojambuliratu yomwe inaonetsedwa m’mipingo yonse pazilumba za ku Indonesia. Anthu 41,265 anaonera pulogalamu yapaderayi. Pa nthawiyi, M’bale Jackson analengeza kuti Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la m’chinenero cha Chisunda litulutsidwa posachedwapa pazipangizo zamakono.
Mabaibulowa amasuliridwa chifukwa cha khama lomwe omasulira anali nalo polimbikira kugwira ntchitoyi kwa zaka zopitirira zitatu ndi hafu. Anthu oposa 100 miliyoni amayankhula chinenero chimodzi kapena zingapo mwa zinenero 4 zomwe zalandira Mabaibulo atsopanowa. Komanso ofalitsa oposa 2,600 amagwiritsa ntchito zinenerozi mu utumiki komanso pamisonkhano yampingo.
Anthu ambiri masiku ano samamva mawu ovuta omwe anagwiritsidwa ntchito m’Mabaibulo akale. Mmodzi mwa omasulira anati: “Kukhala ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lathunthu lomwenso ndi lamakono kukunditsimikizira kuti Yehova akufuna kuti munthu aliyense amve Mawu ake m’chinenero chosavuta kumva komanso chomufika pamtima.”
A Daniel Purnomo a mu Komiti ya Nthambi ya ku Indonesia anafotokoza kuti: “Tikukhala m’nthawi zovuta, makamaka chifukwa cha mliri wa COVID-19. Abale ndi alongo athu okondedwa amene amalankhula zinenerozi asangalala kwambiri kulandira mphatso yauzimu imeneyi yomwe yafika pa nthawi yoyenera.”
Tikusangalala kuti Yehova wachititsa kuti anthu ambiri alandire mphatso yamtengo wapatali ya Mawu ake. Tikukhulupirira kuti anthu ambiri amene amalankhula zinenerozi apindula kwambiri ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.—Yakobo 1:17.