Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Daniel Hutabarat ndi Wilhinson Sihotang aima patsogolo pa Nyumba ya Ufumu ku Batam, Riau Islands

FEBRUARY 26, 2020
INDONESIA

Bungwe la Maphunziro Lalemekeza Ufulu Wachipembedzo wa Anyamata Awiri

Bungwe la Maphunziro Lalemekeza Ufulu Wachipembedzo wa Anyamata Awiri

Pa 22 January 2020, bungwe loyang’anira maphunziro ku Indonesia linalamula kuti achinyamata a Mboni za Yehova awiri omwe mayina awo ndi Daniel Hutabarat komanso Wilhinson Sihotang, abwezeretsedwe sukulu mwamsanga. Anyamata awiriwa anachotsedwa sukulu pa 29 November 2019, chifukwa choti anakana kuchitira sawatcha mbendera komanso kuimba nyimbo ya fuko. Iwo anakana kuchita zimenezi chifukwa choti n’zosemphana ndi zimene amakhulupirira. Anyamatawa anabwereranso kusukulu pa 23 January 2020.

Bungwe loyang’anira maphunziroli litaunikanso nkhaniyi, linapeza kuti abale athuwa amalemekeza akuluakulu a pasukulupo ndiponso boma. Kungoti samafuna kuchita zinthu zilizonse zimene zingasemphane ndi mfundo zomwe amaphunzira m’Baibulo. M’bale Yoga Sulistiono, yemwe amayang’anira Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku nthambi ya Indonesia anati: “A Mboni za Yehova akuyamikira zimene bungweli lanena ndipo akuthokoza akuluakulu omwe amalemekeza ufulu wathu wachipembedzo.”

Koposa zonse, tikuthokoza Yehova, yemwe ndi Mlangizi Wathu Wamkulu chifukwa cha nkhani yosangalatsa imeneyi.—Yesaya 30:20.