6 JUNE, 2022
INDONESIA
Mabuku a Mateyu ndi Maliko Atulutsidwa M’chilankhulo Chamanja cha ku Indonesia
Pa 29 May 2022, M’bale Daniel Purnomo wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Indonesia, anatulutsa mabuku a m’Baibulo a Mateyu ndi Maliko m’Chilankhulo Chamanja cha ku Indonesia. Mabuku a m’Baibulowa ogwiritsa ntchito pazipangizo zamakono, anatulutsidwa pamsonkhano womwe unachita kujambulidwa, ndipo anthu 2,127 anamvetsera msonkhanowu.
Mboni za Yehova zinakhazikitsa mpingo woyamba wachilankhulo chamanja cha ku Indonesia pa 14 September 2007, mumzinda wa Jambi ku Sumatra. Kenako mu 2011, a Mboni za Yehova anamasulira mabuku atatu m’Chilankhulo Chamanja cha ku Indonesia. Mabuku ake ndi: Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha komanso lakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! Mu 2011 momwemo, dera loyambirira la chilankhulo chamanja linakhazikitsidwa m’dzikolo, ndipo linali lokwana makilomita 3,000. Chifukwa chakuti panali anthu ambiri omwe amafunikira mabuku a m’Chilankhulo Chamanja cha ku Indonesia, mu 2015, kunakhazikitsiwa ofesi yoti izimasulira mabukuwa. Panopo ku Indonesia kuli mipingo 12 yachilankhulo chamanja komanso magulu 28 ndi timagulu tina ting’onoting’ono.
Mabuku a Mateyu ndi Maliko ndi mabuku oyambirira a m’Baibulo omwe amasuliridwa m’Chilankhulo Chamanja cha ku Indonesia. Munkhani yake potulutsa Baibuloli, M’bale Purnomo ananena kuti: “Mabuku a m’Baibulowa amasuliridwa bwino kwambiri ndipo akuthandizani kumvetsa bwino moyo wa anthu otchulidwa m’Baibulo.”
Mmodzi mwa ogwira ntchito yomasulira mabuku anati: “Baibuloli lindithandiza kuphunzira zambiri zokhuza Yesu, ngati kuti ndikulankhulana naye pamasom’pamaso.”
Pemphero lathu ndi lakuti Baibuloli lithandize onse amene amagwiritsa ntchito Chilankhulo Chamanja cha ku Indonesia kuti apitirize kuliona ngati ‘nyale yowaunikira kumapazi, komanso kuwala kowaunikira njira.’—Salimo 119:105.