Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

3 FEBRUARY, 2021
INDONESIA

Madzi Oopsa Anasefukira ku Indonesia

Madzi Oopsa Anasefukira ku Indonesia

Malo

Ku South Kalimantan, North Sulawesi, ndi ku North Moluccas

Tsoka lomwe linachitika

  • Mkatikati mwa January 2021, kunasefukira madzi oopsa komanso nthaka inagumuka. Zimenezi zinachititsa kuti zinthu zambiri ziwonongeke komanso anthu ambiri asowe pokhala

Mmene zinakhudzira abale ndi alongo athu

  • Ofalitsa pafupifupi 90 anasamuka m’nyumba zawo kwakanthawi

Kuwonongeka kwa katundu

  • Nyumba zitatu zinawonongeka pang’ono

Ntchito yothandiza kukachitika ngozi

  • Akulu anachita zinthu mofulumira pothandiza ofalitsa kuti asamuke. Akulu anaonetsetsanso kuti abale ndi alongo apeza malo okhala, chakudya ndi zinthu zina zofunika

  • Abale ndi alongo a m’deralo akuthandiza pantchito yoyeretsa ndi kukonza nyumba zowonongeka

  • Oyang’anira madera akulimbikitsa mwauzimu abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi

  • Pogwira ntchitoyi, abale ndi alongo, anatsatira malangizo opewera matenda a COVID-19

Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa abale achikondi omwe ndi okonzeka kuthandiza “pakagwa mavuto.”​—Miyambo 17:17.