JUNE 24, 2021
INDONESIA
Ntchito Yopereka Thandizo ku Indonesia Inalimbitsa Chikondi cha Abale ndi Alongo Komanso Kupereka Umboni Wabwino
Pa 4 April 2021, mphepo yankutho yotchedwa Seroja inawononga kwambiri ku Indonesia. Ndiyeno panakhazikitsidwa ntchito yopereka nthandizo moti nyumba za abale zomwe zinawonongeka zinakonzedwanso. Koposa zonse, ntchitoyi inalimbitsa chikondi pakati pa abale komanso kuthandiza anthu ena omwe anaona zimene zinachitika, kutamanda Yehova.
Mlongo Ela Ludjipau yemwe akulera yekha ana, nyumba yake yomwe inawonongeka anaikonzanso. Amene ankatsogolera ntchito yopereka thandizoyi anali a Komiti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi (DRC). Mlongo Ela anati: “Ngakhale kuti ndimakhala ndekha ndi ana anga, sindidziona kuti ndili ndekha chifukwa abale ndi alongo anga amandithandiza nthawi zonse.” Mlongo winanso dzina lake Yuliana Baunsele anati: “Nditaona abale akubwera kudzandithandiza ngoziyi itangochitika kumene, zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro chimene ndinali nacho chakuti Yehova amandisamalira.”
M’bale Dicky Thome mmodzi wa a Mkomiti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi, anati: “Zinali zosangalatsa kuona Yehova akuthandiza abale ndi alongo amene ankafunikira thandizo. Zinali zolimbikitsa kuona abale ndi alongo amene anathandizidwawo akusangalala komanso kuyamikira. Chikhulupiriro chathu chinalimba chifukwa tinaona kuti abale ndi alongowo ankakhulupirira kuti Yehova awateteza komanso awathandiza.”
Koma si abale ndi alongo okha amene anaona kuti timakondana. M’bale Marsel Banunaek ndi banja lake amakhala m’dera limene anthu ake amasankhana mitundu. Maneba ake amatsutsa kwambiri a Mboni za Yehova. Koma Banunaek ananena kuti maneba ataona abale ndi alongo a mitundu yosiyanasiyana akubwera kudzapereka thandizo kubanja lawo, ena anamuuza kuti: “A Mboni za Yehova amachita zosiyana kwambiri ndi zimene tinamva.” M’bale Banunaek anafotokoza kuti: “Maneba athu anadabwa kwambiri ataona kuti ndife anthu okondana ndiponso ogwirizana. Komanso achibale athu anaona kuti abale ndi alongo ndi anthu achifundo. Panopa achibalewa amatifunsa mafunso okhuda zimene timakhulupirira. Timathokoza kwambiri chifukwa cha chikondi chimene abale ndi alongo padziko lonse tili nacho.”
Mayi wina wogwira ntchito zaboma dzina lake Yosi Duli Ottu, ananena kuti a Mkomiti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi anachita zinthu mwapadera kwambiri chifukwa anakonzekera bwino komanso ankatsatira malamulo onse opewera mliri wa COVID-19. Polankhula ndi a mkomitiyi, iye anati: “Ndachita chidwi kwambiri ndi zimene mwachitira anzanuwa. Mwachita zinthu mofulumira kwambiri kudzawathandiza atakumna ndi tsokali. Muli ndi dongosolo labwino lothandizira anthu pakachitika ngozi zadzidzidzi ndiponso muli ndi zonse zofunikira pa ntchitoyi.”
Ngozi zadzidzidzi zikhoza kuononga zinthu koma sizingaononge chikondi chachikhristu komanso m’gwirizano. Timasangalala kwambiri kuona kuti ‘ntchito zabwino’ zikulimbitsa chikondi chimene tili nacho kwa abale ndi alongo athu ndiponso zikuthandiza anthu ena ‘kulemekeza’ Yehova.—Mateyu 5:16.