Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 23, 2018
INDONESIA

Zivomezi Zawononga pa Chilumba cha ku Indonesia

Zivomezi Zawononga pa Chilumba cha ku Indonesia

Chakumapeto kwa mwezi wa July ndi kumayambiriro kwa August, zivomezi zingapo zinagwedeza chilumba cha Lombok ku Indonesia ndipo anthu osachepera 436 anafa komanso anthu pafupifupi 350,000 anasamuka m’nyumba zawo. Chivomezi china champhamvu chinagwetsa nyumba komanso chinawononga katundu wa ndalama madola mamiliyoni ochuluka.

Ngakhale kuti nyumba zina za ofalitsa zinaonongeka, malipoti ochokera ku ofesi ya nthambi ku Jakarta akusonyeza kuti palibe wa Mboni yemwe anavulala kapena kufa. Komanso, pachilumbapa pali mpingo umodzi wokha wa ofalitsa 40 ndipo nyumba yomwe ankachitiramo misonkhano inawonongeka. Abale awiri oimira ofesi ya nthambi anapita ku malo amene chivomezichi chinawononga kuti akaone chithandizo chomwe angafunike kupereka komanso kutonthoza anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi.

Tipitiriza kupempherera abale athu pa nthawi yovutayi chifukwa tikudziwa kuti Yehova ‘awatonthoza m’masautso awo onse.’—2 Akorinto 1:4.