Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 21, 2020
ISRAEL

Baibulo Lomasulira Malemba Achiheberi Linatulutsidwa Pamsonkhano Wapadera ku Israel

Baibulo Lomasulira Malemba Achiheberi Linatulutsidwa Pamsonkhano Wapadera ku Israel

Bambo ndi mayi, limodzi ndi ana awo awiri, akusangalala atalandira Baibulo latsopano

“Bungwe Lolamulira linakukonzerani mphatso yapadera.” Umu ndi mmene M’bale Geoffrey Jackson yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira anayambira nkhani yake pamene ankatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achiheberi m’chinenero cha Chiheberi chamakono. Msonkhanowu unachitika pa 11 January 2020, ku Romema Arena, mumzinda Haifa ku Israel ndipo abale ndi alongo 2,125 anapezekapo.

M’bale David Simozrag, yemwe amayang’anira Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku nthambi ya Israel, anati: “M’gawo lathu, muli anthu oposa 8 miliyoni omwe amalankhula Chiheberi. Tikukhulupirira kuti Baibulo la Tanakh a lomwe lamasuliridwa m’Chiheberi chamakono lithandiza kwambiri anthu onsewo.” Baibulo latsopanoli ndi limodzi mwa Mabaibulo ochepa kwambiri omwe anamasuliridwa m’Chiheberi chamakono.

Panopa, Baibulo la Dziko Latsopano likupezeka lathunthu kapena mbali zake zina m’zinenero 186. Mofanana ndi Amasorete omwe anakopera Malemba Achiheberi kalekale, abale athu omwe anagwira ntchito yomasulira Baibulo la Chiheberi anayesetsa mwakhama kuti amasulire uthenga wa m’Baibulo molondola. Ntchito yomasulira Baibuloli inatenga zaka zoposa zitatu. Mmodzi mwa omasulirawa anati: “Anthu ambiri omwe amawerenga Baibulo m’Chiheberi ankadalira mabuku kapena Mabaibulo a zinenero zina pofuna kumvetsa mavesi enaake kapenanso buku lonse la m’Baibulo. Baibulo lamakonoli liwathandiza kuti asamavutike kumvetsa tanthauzo la Malemba.”

Banja lanyamula Baibulo la Chiheberi latsopano lomasuliridwa m’Chiheberi chamakono

M’bale wina anati: “Kwa zaka zambiri, anthu wamba akhala akuvutika kumvetsa mbali yaikulu ya Baibulo la Chiheberi koma panopa munthu wamba azitha kumvetsa uthengawo mosavuta komanso molondola.” N’zosakayikitsa kuti ofalitsa 603 omwe amalankhula Chiheberi pa ofalitsa 2,000 omwe ali m’gawo la nthambi ya Israel, agwiritsa ntchito mphatso yapaderayi “kuti aphunzire chilamulo cha Yehova ndi kuchichita.”—Ezara 7:10.

a Tanakh ndi mawu achidule omwe anapangidwa kuchokera ku magawo atatu a Malemba Achiheberi. M’chiheberi, Malemba Achiheberi anaikidwa m’ndondomeko yosiyana ndi Mabaibulo ambiri. Magawowa ndi: Torah (Chilamulo), Nevi’im (Aneneri) komanso Ketuvim (Mabuku). Mawu akuti Tanakh anapangidwa pophatikiza zilembo zoyambirira za mayina a magawo amenewa. Baibulo la Chiheberi latsopanoli lamasuliridwa motsatira ndondomeko imeneyi.