21 MAY 2021
ISRAEL
Zipolowe za ku Israel ndi ku Palestine
Malo
Israel ndi Palestine
Ngozi yake
Pa 10 May, 2021, anthu ambiri anavulala ku Israel ndi ku Palestine chifukwa cha zipolowe zimene zinayamba ndi anthu okhala ndi zida.
Zipolowezi zachititsa kuti nyumba ndi katundu ziwonongeke m’matauni a ku Israel kumene kumakhala Ayuda ndi Aluya
Mmene zakhudzira abale ndi alongo
Ku Israel ndi ku Palestine kuli ofalitsa oposa 2,000 koma pa onsewa palibe amene wavulala
Ofalitsa 73 anasamuka kwawo kuphatikizapo atumiki a nthawi zonse apadera okwana 15. Atumiki a pa Beteli okwana 13 anafunika kusamuka kaye kuti azikakhala pamalo ena okhala ndi pothawirapo ngati kwaphulika bomba
Zinthu zimene zawonongeka
Nyumba 6 zawonongeka pang’ono
Ntchito yothandiza anthu
Komiti yothandiza anthu ikugwira ntchito limodzi ndi oyang’anira madera ndiponso akulu kuti athandize anthu
Oyang’anira madera akugwiranso ntchito ndi akulu polimbikitsa ofalitsa mwauzimu
Pothandiza anthuwa, aliyense akutsatira njira zopewera matenda a COVID-19
Misonkhano ya mpingo sinasokonezeke chifukwa chakuti ikuchitika pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Pa 15 May, abale ndi alongo anaonera msonkhano wadera pogwiritsa ntchito JW Stream–Studio. Chigawo cha masana chinasokonezedwa katatu chifukwa cha maalamu amene akuluakulu a boma ankaliza. Alamu ikalira, abale ndi alongo ankathawira pamalo abwino kuti atetezeke monga pansi pa masitepe okwerera m’mwamba kapena m’malo oteteza anthu pakaphulika bomba. Ngakhale kuti panali zipolowezi, ofalitsa okwana 804 analumikiza nawo msonkhanowu. Panalinso ofalitsa 297 amene anaonera msonkhanowu mu Chitagalogi. Msonkhano wina wadera wa anthu a m’mipingo 5 ya Chiarabu ku Israel ndi ku Palestine unali pa 22 May.
Abale ndi alongo athu amene akhudzidwa ndi mavuto amenewa akupitiriza kudalira Yehova monga pothawirapo pawo.—Salimo 91:1, 2, 5.