Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

(Kumanzere) Banja lanyamula makadi osonyeza mawu ndi Malemba olimbikitsa kuti akagawire abale ndi alongo mumpingo wawo. (Kumanja m’mwamba) Mlongo yemwe ndi mpainiya akuphunzira Baibulo ndi munthu polumikizana naye kudzera pa vidiyo. (M’munsi Kumanja) Banja lalumikiza misonkhano yampingo pogwiritsa ntchito pulogalamu yochitira misonkhano kudzera pa vidiyo

APRIL 9, 2020
ITALY

Abale ndi Alongo ku Italy Akuyesetsa Kukhalabe Olimba Mwauzimu Ngakhale Kuli Mliri Woopsa

Abale ndi Alongo ku Italy Akuyesetsa Kukhalabe Olimba Mwauzimu Ngakhale Kuli Mliri Woopsa

Dziko la Italy ndi limodzi mwa mayiko omwe muli anthu ambiri omwe apezeka ndi matenda a COVID-19. Ofesi ya nthambi ya ku Italy ikupereka chithandizo komanso ikulimbikitsa abale ndi alongo mogwirizana ndi malangizo omwe Bungwe Lolamulira lapereka.

Makomiti atatu opereka chithandizo pakagwa mavuto adzidzidzi akuthandiza abale m’madera akumpoto, pakati ndi kum’mwera kwa dziko la Italy. Makomitiwa akumadziwa zimene ofalitsa amene akhudzidwa ndi mliriwu akufunikira kudzera kwa oyang’anira madera omwe akumalakhulana pafupipafupi ndi akulu a m’maderawa.

Kuwonjezera pamenepa, akulu m’maderawa akuthandiza ofalitsa kuti azipitirizabe kulalikira komanso kupezeka pamisonkhano. Woyang’anira dera wina, M’bale Villiam Boselli yemwe amatumikira kufupi ndi mzinda wa Milan, womwe unali umodzi mwa mizinda yoyambirira kukhudzidwa ndi mliriwu, anati: “Ngakhale kuti sakuchoka m’nyumba zawo, abale ndi alongo onse akupitirizabe kulumikizana. Komanso akumachita misonkhano polumikizana kudzera pa vidiyo ndipo onse akumalimbikitsana komanso akumakwanitsa kupereka ndemanga zawo. Nawonso abale ndi alongo achikulire akupindula kwambiri ndi njira imeneyi. Ndikuona kuti panopa abale ndi alongo m’mipingoyi ndi ogwirizana kwambiri kuposa kale.”

Komanso, anthu ambiri omwe si Mboni akumaonera misonkhano pamodzi ndi mabanja awo a Mboni. Mlongo wina anati: “Mwamuna wanga sankafuna ngakhale pang’ono kupezeka pamisonkhano koma panopa misonkhano ikuchita kumupeza kunyumba . . . ndipo panopa akusangalala kwambiri kupezeka pamisonkhanoyi.”

Abale ndi alongo akugwiritsa ntchito mpata uliwonse womwe ungapezeke kuti alalikire. Mwachitsanzo, mlongo wina ali pagalimoto popita kukasiya njinga ya olumala kunyumba ya mlongo wachikulire, apolisi atatu anamuimitsa pamalo ochitira chipikisheni. Mlongoyo anafotokoza kuti akukathandiza mzimayi wina wachikulire ndipo anawaonetsa chikalata chomuloleza kuyenda. Kenako anawapatsa timapepala takuti, Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo? ndiponso kakuti, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi? Apolisiwo analandira timapepalato. Pobwerera kokasiya njinga ija, apolisi aja anamuimitsanso. Apolisiwo anayamikira mlongoyo komanso ananena kuti akufuna kudziwa zambiri zokhudza zimene Baibulo limanena pankhani yokhala ndi chiyembekezo. Apolisiwo anaitaniranso anzawo ena awiri kuti amvetsere nawo. Mlongo wathuyu anasangalala kuwaonetsa webusaiti ya jw.org. Wapolisi wina anati: “Zikomo kwambiri madamu, mwatithandiza kuti tikhale osangalala lero.”

M’bale Boselli anati: “Ngakhale kuti udindo wanga wina ndi kulimbikitsa komanso kutonthoza ena, ndalimbikitsidwa kuona abale anga akupitirizabe kukhala olimba mwauzimu ndiponso sakusiya kulambira Yehova. N’zolimbikitsa kwambiri kuona akukonda Yehova ndi mtima wonse ndipo zimenezi zandikhudza kwambiri. Iwo ndi mphatso yofunika kwambiri yochokera kwa Yehova!”

Zikuonekeratu kuti ngakhale kuti pali mavuto aakulu, abale athu akupitirizabe kukhala olimba mwauzimu ndipo ‘sanapatutsidwe ndi masautso amenewa.’​—1 Atesalonika 3:2, 3.