Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nyumba yotchedwa Palace of Justice ku Rome yomwe muli Khoti Lalikulu Kwambiri la Apilo ku Italy

OCTOBER 1, 2019
ITALY

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Italy Lagamula Kuti Makolo Ali ndi Ufulu Wofanana Pophunzitsa Ana Awo Mfundo za Chipembedzo

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Italy Lagamula Kuti Makolo Ali ndi Ufulu Wofanana Pophunzitsa Ana Awo Mfundo za Chipembedzo

Pa 30 August, 2019, Khoti Lalikulu Kwambiri la Apilo ku Rome lomwe ndi lamphamvu kwambiri m’dziko la Italy, linapereka chigamulo chosaiwalika pa mlandu wokhudza woyenera kulera ana komanso ufulu wa makolo. Khotili linagamula kuti mayi wina yemwe ndi wa Mboni za Yehova ali ndi ufulu wophunzitsa mwana wake wamng’ono mfundo za chipembedzo chake.

Bambo a mwanayo omwe si a Mboni za Yehova anapatukana ndi mayi a mwanayo ndipo anakakamira kuti mwanayo aziphunzitsidwa mfundo za chipembedzo cha bambo ake zokha. Makhoti ang’onoang’ono awiri anagamula nkhaniyi mokomera bamboyo ndipo ananena kuti kuphunzitsa mwanayo mfundo za chipembedzo china kukhoza “kumusokoneza.” Zimene makhotiwa anagamula zinkalepheretsa mayiyu kuphunzitsa mwana wake mfundo za chipembedzo chake ngakhale kuti anali ndi ufulu womuphunzitsa. Khoti Lalikulu Kwambiri linagamula mosiyana ndi makhoti ang’onoang’ono ndipo linanena kuti mwanayo ali ndi ufulu “wophunzitsidwa mfundo za chipembedzo ndi makolo onse awiri.” Khotili linanenanso kuti “malamulo a m’dzikoli sakondera chipembedzo chinachake” ndipo linadzudzula zomwe linati ndi “tsankho” lomwe makhoti ang’onoang’ono anachitira a Mboni za Yehova. Popereka chigamulochi, khotili linanenso kuti makolo akasemphana maganizo pa nkhani yophunzitsa ana awo mfundo za chipembedzo, woweruza alibe ufulu wogamula kuti chipembedzo chabwino ndi chiti.

Tikukhulupirira kuti chigamulo cha Khotili, chidzathandiza makhoti ena a ku Italy pogamula milandu inanso yokhudza woyenera kulera ana. Sitikukayikira kuti chigamulochi chithandiza kwambiri makolo amene akuyesetsa kulera ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”—Aefeso 6:4.