Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Khoti la Apilo ku Rome

FEBRUARY 7, 2020
ITALY

Khoti la Apilo ku Rome Lagwirizana ndi Zoti Makolo Ali ndi Ufulu Wosankhira Ana Awo Chithandizo cha Mankhwala Popanda Kugwiritsa Ntchito Magazi

Khoti la Apilo ku Rome Lagwirizana ndi Zoti Makolo Ali ndi Ufulu Wosankhira Ana Awo Chithandizo cha Mankhwala Popanda Kugwiritsa Ntchito Magazi

Pa 17 December 2019, Khoti la Apilo ku Rome, linasintha chigamulo chimene khoti loweruza milandu yokhudzana ndi ana linapereka. Khotili linalanda mlongo wathu mwana chifukwa chakuti sanalole kuti mwanayo aikidwe magazi. Khoti la Apilo linabwezera mlongoyu mwana wake ndipo linagamula kuti alibe mlandu uliwonse. Chigamulochi chithandiza kwambiri pa milandu yotereyi m’tsogolomu komanso chithandiza kuti makolo a Mboni asalandidwe ana awo chifukwa chosankha kuti ana awowo asalandire magazi.

Mlanduwu unayamba mlongo wathuyu ndi mwana wake wa zaka 10 atachita ngozi ya galimoto. Mwanayo anavulala ndipo anapita naye kuchipatala. Patapita masiku atatu, madokotala anakonza zoti amupange opaleshoni. Mlongoyu analola kuti madokotala amupange opaleshoni mwanayo koma anawafotokozera kuti asamuike magazi. Ngakhale kuti mwanayu sanavulale kwambiri moti n’kufunikira magazi, madokotala analembera loya kuti awapatse chilolezo. Iwo ananena kuti mlongoyu sakufuna kuthandiza mwana wakeyo potsatira zimene amakhulupirira kuchipembedzo chawo. Ndiyeno anapempha loyayo kuti awalole kupereka magazi kwa mwanayo. Loyayu ananena kuti mlongo wathuyu ndi wolakwa chifukwa sakufuna kuthandiza mwana wake ndipo anapempha khoti limene limaweruza milandu yokhudza ana kuti limulande mwanayo. Khotili linagwirizana ndi zomwe loyayo ananena ngakhale kuti malamulo salola khotili kupereka chigamulo choterechi. Komabe mlongoyu anakachita apilo za nkhaniyi ku Khoti la Apilo.

Khoti la Apilo linapeza kuti mlongo wathuyu ndi mayi wabwino komanso wachikondi. Chigamulo chomwe khotili linapereka chinafotokoza kuti “si zomveka kunena kuti mayiyu sakonda mwana wake chifukwa choti anakana kulandira magazi potsatira zimene amakhulupirira.” Choncho, khotili linabwezera mlongoyu mwana wake ndipo linanena kuti kumulanda mwanayo kunali kuphwanya malamulo.

Nicola Colaianni, yemwe anali mlangizi wa Khoti Lalikulu Kwambiri la Apilo komanso pulofesa wa malamulo a zipembedzo zachikhristu payunivesite ya Bari anati: “Ndikugwirizana ndi zimene Khoti la Apilo lagamula. Ndikudabwa kwambiri ndi zimene khoti loweruza milandu yokhudzana ndi ana linagamula. Zikuoneka kuti anthu ambiri alibe ufulu weniweni wa chipembedzo ndipo makamaka a Mboni za Yehova.”

M’bale Christian Di Blasio, yemwe amagwira ntchito mu Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku Italy, anati: “Tikuthokoza Khoti la Apilo posintha chigamulo chimene chinaperekedwa chifukwa chodana ndi chipembedzo cha Mboni za Yehova. A Mboni za Yehova amakonda komanso kusamalira bwino ana awo ndipo amayamikira madokotala amene amalemekeza chikumbumtima chawo, powapatsa chithandizo choyenera.”

Chigamulo cha khotili chikunena momveka bwino kuti abale ndi alongo athu ali ndi ufulu wosankha chithandizo cha mankhwala chimene ana awo ayenera kulandira. Tikuthokoza Mulungu wathu Yehova chifukwa chotithandiza kuwina mlanduwu, ndipo zimenezi zithandiza olambira anzathu akamasankha chithandizo cha mankhwala mogwirizana ndi chikumbumtima chawo.—Salimo 37:28.