Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 1, 2016
ITALY

Zivomerezi Zoopsa Zimene Zinachitika M’chigawo Chapakati ku Italy

Zivomerezi Zoopsa Zimene Zinachitika M’chigawo Chapakati ku Italy

M’mawa wa pa 30 October, 2016, m’chigawo chapakati cha dziko la Italy kunachitika chivomezi champhamvu 6.6. Chivomerezi china champhamvu kwambiri chinachitika m’chaka cha 1980 ndipo ichi chinali chachiwiri kuchitika kuchokera m’chaka chimenechi. Anthu osachepera 20 anavulala ndipo malipoti akusonyeza kuti palibe omwe anafa.

Chivomerezicho chinayambira pafupi ndi tauni ya Norcia, ndipo kutangotsala masiku ochepa kuti chichitike, m’derali munachitikanso zivomerezi zina ziwiri. Madzulo a pa 26 October, 2016, chivomerezi champhamvu 5.5 chinachitika ndipo patangotha maola awiri chivomerezi chinanso champhamvu 6.1 chinachitika.

Dera lomwe kunachitika chivomerezichi ndi loyandikana ndi dera lomwenso kunachitika chivomerezi china chimene chinapha anthu pafupifupi 300 pa 24 August 2016.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Italy inanena kuti palibe munthu wa Mboni yemwe anafa kapena kuvulala kwambiri. Komabe mabanja awiri nyumba zawo zinawonongeka ndi chivomezi cha pa 26 October komanso nyumba zambiri za a Mboni ena zinawonongeka. Akulu a m’mipingo ya m’derali anayesetsa kufufuza kuti adziwe zinthu zomwe anthuwa ankafunikira komanso zinthu zomwe zinawonongeka. Zimenezi zinali zofunika chifukwa choti anthu ena anali akuvutikabe chifukwa cha chivomerezi chomwe chinachitika mu August. Mofanana ndi aliyense amene anakhudzidwa ndi ngoziyi, a Mboni ambiri ankachita mantha kugona m’nyumba zawo chifukwa ankaona kuti mwina zikhoza kugwa mosavuta ndi zivomerezi. Chifukwa cha zimenezi ambiri ankagona m’magalimoto, m’matenti komanso m’Nyumba za Ufumu zomwe ndi malo olambirira a Mboni za Yehova.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi limene limayendetsa ntchito yothandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zachilengedwe. Bungweli limagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo pofuna kuthandiza ntchito yolalikira ya padziko lonse. Ku Italy kuli a Mboni oposa 251,000.

Lankhulani ndi:

Padziko Lonse: David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000

Italy: Christian Di Blasio, 39-06-872941