Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nyumba yotchedwa Palace of Justice ku Rome yomwe muli Khoti Lalikulu Kwambiri la Apilo ku Italy

JULY 18, 2019
ITALY

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Italy Lagamula Kuti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wopanga Zosankha pa Nkhani ya Chithandizo Chamankhwala

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Italy Lagamula Kuti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wopanga Zosankha pa Nkhani ya Chithandizo Chamankhwala

Pa 15 May, 2019, Khoti Lalikulu Kwambiri la Apilo ku Italy, lomwe ndi lamphamvu kwambiri m’dzikolo, linagwirizana ndi zoti abale athu ali ndi ufulu wosankha okha chithandizo chamankhwala chomwe akufuna. Khotili linatsimikizira kuti wodwala ali ndi ufulu wosankha munthu womuimira yemwe adzaonetsetse kuti zomwe wodwalayo anasankha zoti asaikidwe magazi zatsatiridwa. Kuwonjezera pamenepo, khotili linatsimikizira kuti malamulo a ku Italy amalola wodwala kusankha munthu womuimira pa thandizo la zachipatala ngakhale zitakhala kuti wodwalayo watsala pang’ono kukomoka, kusiya kulankhula, kapena kusiya kuchita chilichonse.

M’bale ndi Mlongo Cappelli

Khotili linanena zimenezi chifukwa cha nkhani zingapo zomwe zinapita kukhoti zokhudza M’bale Luca Cappelli yemwe amatumikira monga mkulu mumpingo. M’baleyu wakhala akuvutika ndi vuto lokhudza mitsempha ya muubongo kwa zaka 25 zapitazi. Vutoli limachititsa kuti M’bale Cappelli azipatsidwa chithandizo cha kuchipatala chosiyanasiyana komanso nthawi zina amalephera kulankhula. Asanayambe kulandira chithandizo, m’baleyu anasainiratu chikalata chosonyeza thandizo lomwe angalole kupatsidwa komanso lomwe sangalole, ndipo anasankha mkazi wake Francesca kukhala womuimira pa thandizo la zachipatala. Koma woweruza milandu ndiponso khoti la apilo anakana kuti mkazi wa m’baleyu akhale womuimira pa thandizo la zachipatala, zomwe zinatanthauza kuti M’bale Cappelli analibenso njira yovomerezeka ndi malamulo yotsimikizira kuti sadzaikidwa magazi.

Pa 16 February, 2017, mlandu wa M’bale Cappelli unapita ku Khoti Lalikulu Kwambiri la Apilo. Khotili linagamula kuti makhoti aang’ono omwe anazenga mlanduwu anaphwanya zomwe zili m’Malamulo Oyendetsera Dziko la Italy komanso m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Europe, zomwe zimati wodwala ali ndi ufulu wosankha yekha zimene akufuna. N’zochititsa chidwi kuti khotili linanena kuti kukana chithandizo chinachake chamankhwala “ndi ufulu woyenera kutetezedwa kwambiri komanso kuperekedwa kwa wodwala makamaka ngati wodwalayo akukana chifukwa cha zimene amakhulupirira ku chipembedzo chake.” Chifukwa cha chigamulo cha Khoti Lalikulu Kwambiri chimenechi, makhoti a ku Italy tsopano ayenera kumalemekeza kwambiri zomwe abale athu amasankha pofuna kupewa kuikidwa magazi.

A Mboni za Yehova padziko lonse akusangalala kuti Khoti Lalikulu Kwambiri lachitapo kanthu pofuna kuteteza ufulu wa abale athu ku Italy, omwe akupitirizabe kutsatira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo pa nkhani yogwiritsa ntchito magazi.—Machitidwe 15:29.