Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ofesi ya loya woimira boma pa milandu komanso khoti la m’tawuni ya Termini Imerese ku Sicily m’dziko la Italy.

AUGUST 22, 2018
ITALY

Khoti la ku Sicily Linagamula Kuti Odwala Omwe Ndi a Mboni za Yehova Ali Ndi Ufulu Wosankha Chithandizo cha Mankhwala

Khoti la ku Sicily Linagamula Kuti Odwala Omwe Ndi a Mboni za Yehova Ali Ndi Ufulu Wosankha Chithandizo cha Mankhwala

Pa 6 April, 2018, Khoti la ku Termini Imerese pa chilumba cha Sicily m’dziko la Italy, linagamula kuti dokotala wina wopanga maopaleshoni anapalamula mlandu chifukwa anaika magazi mokakamiza mzimayi wina yemwe ndi wa Mboni za Yehova. Dokotalayo analamulidwa kuti apereke chindapusa kwa mzimayiyu cha ndalama zokwana madola 11,605 a ku America yomwe ndi mbali yoyamba ya ndalama zachipepeso, ndiponso kuti apereke kwa mwamuna wa mayiyu yemwenso ndi wa Mboni za Yehova ndalama zina zokwana madola 5,803 a ku America. Aka ndi koyamba kuti khoti ku Italy ligamule kuti dokotala ndi wolakwa chifukwa chophwanya ufulu womwe munthu aliyense ali nawo wosankha zomwe ziyenera kuchitika pa thupi lake mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.

Mlanduwu ukukhudza mlongo wina yemwe anayamba kudwaladwala atangopangidwa opaleshoni ya ndulu mu December 2010. Mlongoyu anaikidwa maselo ofiira a magazi mochita kumukakamiza ngakhale kuti anakanitsitsa kuti sakufuna kuikidwa magazi. Dokotala yemwe anapanga opaleshoniyo ananama kuti anachita kupatsidwa chilolezo ndi woweruza milandu wina kuti achite zimenezi.

Zimenezi zitachitika, mlongoyu limodzi ndi mwamuna wake anakadandaula za nkhaniyi ku ofesi ya loya woimira boma pa milandu. Khotili linagamula kuti “ngati wodwalayo ndi wa Mboni za Yehova yemwe ndi wamkulu ndipo akhoza kusankha yekha zochita, . . . dokotala ayenera kupewa kumuika magazi” ngati kuchita zimenezi kukusemphana ndi zomwe wodwalayo akufuna.

Khotili linanenanso kuti Malamulo Oyendetsera Dziko la Italy amaletsa madokotala kupereka chithandizo popanda chilolezo ngakhale ataona kuti chithandizocho n’chofunika. Malinga ndi zomwe khotili linagamula, “ngakhale kuti dokotala akhoza kupereka chithandizo kwa wodwala ngati akuganiza kuti n’chofunikiradi, . . . zimenezi n’zosayenera ngati wodwala atanena kuti sakufuna.”

A Daniele Rodriguez ndi pulofesa wa zamalamulo a chipatala komanso woona zinthu zoyenera ndi zosayenera pa nkhani ya zamankhwala pa Yunivesite ya Padua, ndipo analemba lipoti lomwe linagwiritsidwa ntchito pa mlanduwu. Popereka umboni pa mlanduwu, iwo ananena kuti “ufulu wokana chithandizo chinachake cha mankhwala ndi wovomerezeka ndi malamulo oyendetsera dziko ndipo unafotokozedwa momveka bwino mu [gawo] 32 la Malamulo Oyendetsera Dziko [la Italy] omwe amanena kuti ‘munthu aliyense asamakakamizidwe kulandira chithandizo chinachake cha mankhwala pokhapokha ngati malamulo akulola kutero.’” A Luca Benci omwe ndi katswiri wa zamalamulo komanso malamulo a zachithandizo chamankhwala ku Italy, analemba mu magazini ya Quotidiano Sanità (Health Daily) kuti: “Palibe lamulo lomwe limakakamiza kuika magazi odwala omwe sakufuna. Munthu ali ndi ufulu wokana kulandira chithandizo ndipo ufulu umenewu ndi wofunika kuposa chilichonse.”

A Marcello Rifici omwe ndi mmodzi wa maloya oimira Mboni za Yehova anati: “Ndife osangalala chifukwa chigamulochi chikugwirizana ndi mfundo zomwe mayiko a ku Europe amayendera. Zina mwa mfundozi zinafotokozedwa ndi Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe, ndipo zimanena momveka bwino kuti wodwala aliyense ali ndi ufulu wosankha chithandizo chomwe akufuna. N’zochititsa chidwi kuti Nyumba ya Malamulo ku Italy inakhazikitsa lamulo nambala 219/2017 lomwe limatchedwa kuti ‘Living Will Law,’ ndipo limatsindika mfundo zofanana ndi zomwe zili m’chigamulochi.”

A Lucio Marsella omwenso ndi mmodzi wa maloya a Mboni za Yehova anati: “Chigamulochi chithandiza madokotala onse omwe amalimba mtima n’kuyesetsa kupereka chithandizo choyenera kwa odwala, kwinaku akulemekeza ufulu wa odwalawo wosankha chithandizo chomwe akufuna.”