JUNE 27, 2019
ITALY
Madokotala ku Italy Anasonyeza Chidwi pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi
Madokotala ambiri akusangalala ndi zimene gulu lathu likuchita padziko lonse pokhazikitsa njira zosiyanasiyana zothandiza azachipatala kudziwa zomwe angachite pothandiza odwala kapenanso kupanga opaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Dipatimenti Yoyang’anira Zachipatala (Italy), yomwe ili pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Rome, ndi imodzi mwa njira zomwe zinakhazikitsidwa pofuna kuthandiza azachipatala. Kuyambira pa 10 mpaka 13 October, 2018, mumzinda wa Palermo ku Siciliy, kunachitika msonkhano wa akatswiri osiyanasiyana azachipatala. (National Congress of the Italian Society of Anesthesia, Analgesia, Resuscitation, and Intensive Care, SIAARTI) Pamsonkhanowu, abale ena amene ali mu Dipatimenti Yoyang’anira Zachipatala (Italy) komanso mu Komiti Yolankhulana ndi Achipatala, anakhazikitsa malo apadera pomwe ankasonyeza ndi kufotokozera azachipatala njira zosiyanasiyana zothandizira odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi. Msonkhanowu utatha, abalewa anakakhazikitsanso malo ngati omwewa kumsonkhano wa akatswiri enanso azachipatala (Joint Congress of the Scientific Societies of Surgery) womwe unachitikira ku Rome “La Nuvola” Convention Center.
Misonkhano yotereyi imathandiza kuti pa nthawi imodzi, akatswiri ambiri azachipatala adziwe njira zatsopano zokhudza kuthandiza odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi. Pamsonkhano womwe unachitikira ku Palermo panali madokotala 2,800 omwe amapereka mankhwala opangitsa dzanzi odwala akamafuna kupangidwa opaleshoni. Pamsonkhano wa madokotola opanga maopaleshoni womwe unachitika ku Rome, panali madokotala 3,500. Zikuoneka kuti msonkhanowu unali waukulu kwambiri pa misonkhano yonse ya madokotala opanga maopaleshoni yomwe yakhala ikuchitika ku Italy. Madokotala enanso ochokera m’zipatala zosiyanasiyana zodziwika bwino anabwera pamsonkhanowu. Ena mwa madokotalawa anali ochokera m’mabungwe onse a madokotala opanga maopaleshoni ku Italy komanso ochokera ku sukulu yophunzitsa madokotala ya Italy Chapter of the American College of Surgeons. Mabungwe enanso ambiri a m’dzikoli monga Unduna wa Zaumoyo anapezeka kumsonkhanowu.
Dokotala wina wochokera ku chipatala cha Policlinico Hospital of Catania ku Sicily, dzina lake Vincenzo Scuderi, anapezeka pamalo apadera omwe abale anakhazikitsa ku Palermo. Pa 18 January, 2019, dokotalayu anathandiza wa Mboni wina yemwe mtsempha wake waukulu wa mtima unaphulika. Iye anakwanitsa kupanga opaleshoni yovuta kwambiri imeneyi popanda kugwiritsa ntchito magazi. Dokotalayu anafotokoza kuti: “[Malo apadera] omwe munakhazikitsa pamsonkhano wa SIAARTI wa 2018, anali othandiza kwambiri. Zinthu zimene munatipatsa zofotokoza njira zosiyanasiyana zothandizira odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi zinatithandiza kwambiri.”
Panopa, madokotala opitirira 5,000 ku Italy avomereza kuti azithandiza odwala omwe ndi a Mboni za Yehova powapatsa mankhwala komanso kuwapanga opaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Chaka chilichonse ku Italy, odwala a Mboni pafupifupi 16,000 amathandizidwa popanda kugwiritsa ntchito magazi.