Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

23 JANUARY, 2017
ITALY

Ku Central Italy Kunagwa Sinowo Yoopsa

Ku Central Italy Kunagwa Sinowo Yoopsa

Lachitatu pa 18 January, 2017, mu mzinda wa Abruzzo womwe uli pachigawo chapakati cha dziko la Italy, munagwa sinowo yowononga. Chaka chatha mu August, mu derali munachitikanso chivomezi champhamvu chomwe chinakwirira hotelo ina imene inali ndi anthu 30 mkati mwake. Kugwa kwa sinowoyu kunachitika pambuyo pa zivomezi 4 zamphamvu kwambiri zomwe zinachitika m’deralo tsiku lomwelo. Ntchito yopulumutsa anthu amene anakhudzidwa ndi zivomezizo inali yovuta chifukwa chakuti kunagwa sinowo wamphamvu mlungu umodzi ngoziyo isanachitike. Matauni ambiri analibe magetsi komanso anali ovuta kufikako.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Italy inanena kuti ngakhale kuti palibe wa Mboni aliyense amene wafa kapena kuvulala kwambiri, iwo akuyesetsa kukumana ndi mabanja a a Mboni omwe ali m’madera amene anakhudzidwa kwambiri ndi zivomezi komanso sinowo. Akulu a Mboni m’derali akhala akupatsa mabanja okhudzidwa chakudya, madzi, nkhuni, komanso zinthu zina zofunika. Ofesi ya nthambi ikupitiriza kufufuza mmene zinthu zilili komanso kuthandiza anthu okhudzidwa.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Italy: Christian Di Blasio, +39-06-872941