Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 21, 2016
ITALY

A Mboni za Yehova Analimbikitsa Anthu Amene Anakhudzidwa ndi Chivomerezi ku Italy

A Mboni za Yehova Analimbikitsa Anthu Amene Anakhudzidwa ndi Chivomerezi ku Italy

ROME—M’mwezi wa September 2016, a Mboni za Yehova anagawira magazini a Nsanja ya Olonda omwe ankafotokoza za amene angatithandize tikakumana ndi mavuto. Magaziniyo inali ndi mutu wakuti “Kodi Ndi Ndani Angatithandize Tikakhala pa Mavuto?” ndipo inkagawiridwa ndi Mboni za Yehova padziko lonse. A Mboni za Yehova ku Italy anagwira ntchito mwakhama pogawira magaziniyi m’chigawo chapakati cha dzikolo. Pa 24 August 2016, m’chigawochi munachitika chivomerezi champhamvu m’madera a Lazio, Marche ndi Umbria. Anthu pafupifupi 300 anafa ndipo anthu oposa 2,000 anasowa pokhala.

A Christian Di Blasio ndi wofalitsa nkhani wa Mboni za Yehova ku Italy ndipo anafotokoza kuti: “Cholinga chogawira magaziniyi, chinali chofuna kuthandiza anthu omwe akukumana ndi mavuto padziko lonse lapansi. Komabe ku Italy kuno ntchitoyi inathandiza anthu omwe anavutika ndi chivomerezi komanso anthu omwe anathandiza anzawo pa nthawi yatsokali.”

A Mboni za Yehova akulankhula ndi munthu amene anakhudzidwa ndi chivomerezi m’tauni ya Amatrice komwe anthu ambiri anafa.

M’chigawochi muli mipingo 15 ya Mboni za Yehova koma palibe wa Mboni aliyense amene anafa kapena kuvulala modetsa nkhawa pa nthawiyi. Komabe nyumba zitatu za a Mboni zinawonongeka ndipo zina zinagweratu. A Di Blasio ananenanso kuti a Mboni amene nyumba zawo zinagwa anadzipereka kugwira ntchito yapadera yogawira magazini kwa anthu a m’dera lawo. Komanso a Mboni omwe anapulumuka pa tsokali anadzipereka kudzathandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi vutoli. A Di Blasio anafotokoza kuti: “A Mboni omwe anathandiza anzawo ananena kuti uthenga umene ankalalikira unkawalimbikitsa kwambiri ndipo akufunitsitsa kuuza anthu ambiri a m’dera lawo.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000

Italy: Christian Di Blasio, 39-06-872941