Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 20, 2019
JAPAN

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Linatulutsidwa M’Chijapanizi

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Linatulutsidwa M’Chijapanizi

Loweruka pa 13 April, 2019, M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso la chinenero cha Chijapanizi. Baibuloli linatulutsidwa pamsonkhano wapadera womwe unachitikira ku Noevir Stadium Kobe mumzinda wa Kobe ku Japan ndipo pamsonkhanowu panali anthu 20,868. Anthu enanso anaonera msonkhanowu m’Malo a Misonkhano 8 komanso m’Nyumba za Ufumu zambiri m’gawo la nthambi ya Japan pa nthawi yomwe msonkhanowu unkachitika. Vidiyo yojambulidwa ya msonkhanowu inaonetsedwa tsiku lomwelo msonkhanowu utatha komanso tsiku lotsatira m’Nyumba za Ufumu zomwe anthu sanathe kuonera msonkhanowu pa nthawi yomwe unkachitika. Anthu onse omwe anaonera komanso kupezeka pamsonkhano wapaderawu anakwana 220,491.

Sitediyamu ya Noevir Stadium Kobe

Padziko lonse pali timagulu, magulu komanso mipingo ya Chijapanizi yoposa 2,950. Tikusangalala kuti abale athu oyankhula Chijapanizi panopa ali ndi Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso lomwe ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo liwathandiza pophunzira paokha ndiponso polalikira mogwira mtima.—Aheberi 4:12.

Abale ndi alongo akusangalala kulandira Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso lawolawo.

Baibulo la Dziko Latsopano linayamba kutulutsidwa ku Japan zaka 45 zapitazo. Mu 1973, M’bale Lyman Swingle yemwe anali m’Bungwe Lolamulira, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu pamsonkhano wamayiko wakuti “Kupambana kwa Mulungu,” womwe unachitikira mumzinda wa Osaka ku Japan. Pambuyo pa zaka 9 chitulutsireni Baibuloli, Mabaibulo 1,140,000 anali atagawidwa ndipo chiwerengerochi chinali choposa chiwerengero cha ofalitsa maulendo pafupifupi 75 omwe anali ku Japan pa nthawiyo. Mu 1982, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lathunthu linatulutsidwa. Ntchito yosindikiza komanso kumanga pamodzi mapepala a Baibuloli inachitikira ku Japan. Chaka cha 2019 ndi chaka chinanso chosaiwalika kwa anthu a Yehova ku Japan chifukwa cha kutulutsidwa kwa Baibulo lokonzedwanso limeneli.

Baibulo la Dziko Latsopano lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’zinenero 179 kuphatikizapo Mabaibulo a zinenero 22 omwe akonzedwanso mogwirizana ndi la Chingelezi lomwe linatulutsidwa mu 2013.