Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

4 JANUARY 2024
JAPAN

Chivomerezi Champhamvu Chawononga pa Gombe la Noto ku Japan

Chivomerezi Champhamvu Chawononga pa Gombe la Noto ku Japan

Pa 1 January 2024, chivomerezi cha mphamvu zokwana 7.6, chinachitika pagombe la Nato m’chigawo chapakati cha Ishikawa ku Japan. Chivomerezichi chinawononga kwambiri zinthu monga nyumba za anthu komanso misewu m’derali. Anthu opitirira 33,000 anathawa m’nyumba zawo. Anthu 400 anavulala pomwe 78 anamwalira.

Mmene Chivomerezichi Chakhudzira Abale ndi Alongo Athu

  • Palibe m’bale kapena mlongo yemwe anamwalira

  • M’bale mmodzi anavulala pang’ono

  • Abale ndi alongo opitirira 150 anathawa m’nyumba zawo

  • Nyumba ziwiri zinagwa

  • Nyumba 7 zinawonongeka kwambiri

  • Nyumba zoposa 100 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba ya Ufumu imodzi inaonongeka kwambiri

  • Nyumba za Ufumu 8 zinaonongeka pang’ono

Ntchito Yopereka Chithandizo

  • Komiti Yothandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi inakhazikitsidwa kuti iyendetse ntchito yopereka chithandizo

  • Abale a ku ofesi ya nthambi ya Japan anatumizidwa kuti akalimbikitse abale ndi alongo athu. Oyang’anira madera komanso akulu nawonso akuyesetsa kulimbikitsa abale omwe akhudzidwa pogwiritsa ntchito Baibulo komanso kuwapatsa zinthu zofunikira

Sitikukayikira kuti Yehova apitiriza kukhala malo “othawirako otetezeka” kwa abale ndi alongo athu ku Japan powatonthoza ndi kuwalimbitsa pa nthawi yovuta kwambiriyi.​—Salimo 18:2.