Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 23, 2019
JAPAN

Mphepo Yamkuntho ya Hagibis Yawomba Posachedwa ku Japan

Mphepo Yamkuntho ya Hagibis Yawomba Posachedwa ku Japan

Kuyambira pa 12 mpaka pa 13 October, 2019, mphepo yamkuntho ya Hagibis inawomba ku Japan ndipo inapha anthu osachepera 77 komanso inachititsa kuti madzi asefukire kwambiri. Nyumba masauzande ambirimbiri zinalibe magetsi kapena madzi a m’mipope. Anthu a ku Japan akupitirizabe kufufuza anthu omwe anasowa. Akatswiri akuti mphepoyi ndi yamphamvu kwambiri pa mphepo zonse zomwe zakhala zikuwomba ku Japan kuyambira m’chaka cha 1958, ndipo inachititsa kuti m’madera ena a m’dzikoli mugwe mvula yamphamvu kwambiri ya mamilimita oposa 889.

Pambuyo pofufuza zokhudza abale athu onse, zapezeka kuti palibe amene waphedwa ndi mphepoyi. Komabe, abale 10 anavulala pang’ono. Kuonjezera pamenepa, nyumba za abale athu zoposa 1,200 zinawonongeka. Nyumba za Ufumu zokwana 23 zinawonongeka ndipo zitatu mwa zimenezi sizikugwiritsidwa ntchito panopa chifukwa cha madzi osefukira kapena chifukwa cha kuzima kwa magetsi. Nyumba ya Msonkhano ya ku Tochigi inawonongekanso pang’ono.

Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi akhazikitsidwa m’madera a Fukushima ndi Nagano. Makomiti enanso akhoza kupangidwa ofesi ya nthambi ikadziwa mmene mphepo yamkunthoyi yawonongera m’madera ena. Abale omwe akhudzidwa ndi mphepoyi akulandira chakudya ndi madzi. Oyang’anira madera apatsidwa ntchito yoti azilimbikitsa komanso kutonthoza abale ndi alongo a m’madera awo pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

Tili ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova apitiriza kukhala pothawirapo pa abale athu pa nthawi yovutayi.—Salimo 142:5.