OCTOBER 10, 2019
JAPAN
Mphepo Yamkuntho ya Tapah Yawononga Kum’mwera kwa Japan
Kuyambira pa 21 mpaka 23 September, 2019, mphepo yamkuntho ya Tapah inawononga kum’mwera kwa dziko la Japan. Mphepoyi inkawomba mwamphamvu kwambiri ndipo inachititsa kuti kugwe mvula yamphamvu. Chifukwa cha mphepoyi maulendo a pandege ndi sitima zapamtunda anaimitsidwa, komanso magetsi anazima m’nyumba zoposa 30,000. Anthu oposa 50 anavulala ku Okinawa ndi ku Kyushu.
Ofesi ya nthambi ya ku Japan yanena kuti ofalitsa 5 anavulala kuphatikizapo mlongo mmodzi yemwe anagonekedwa m’chipatala. Nyumba za abale athu zoposa 50 zinaonongeka. Komiti Yothandiza Pangozi Zogwa Mwadzidzidzi ndi akulu ena akuthandiza ofalitsa amene akhudzidwa ndi mphepo yamkunthoyi powapatsa chakudya ndi pokhala komanso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo. Ofesi ya nthambi ya ku Japan ipitiriza kufufuza mmene mphepoyi yakhudzira ofalitsa ndi kuwapatsa chithandizo choyenerera.
Tikupemphera kuti abale athu a ku Japan apitirize kudalira Yehova kuti aziwatonthoza pa nthawi yovutayi.—Salimo 94:19.