Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 12, 2018
JAPAN

Madzi Osefukira Anawononga Kumadzulo kwa Dziko la Japan

Madzi Osefukira Anawononga Kumadzulo kwa Dziko la Japan

M’chigawo cha kumadzulo kwa dziko la Japan, anthu osachepera 169 anafa komanso ena oposa 255,000 akusowabe madzi m’nyumba zawo chifukwa cha mvula yamphamvu yomwe inachititsa kuti madzi asefukire n’kuwononga zinthu ndiponso kugumula nthaka.

Ngakhale kuti palibe wa Mboni za Yehova aliyense yemwe wafa pa ngoziyi, a Mboni 200 anasamutsidwa ndipo mlongo m’modzi anavulala. Mlongoyu analandira thandizo kuchipatala ndipo panopa akupezako bwino. Nyumba za abale athu zosachepera 103 zinaonongeka ndipo imodzi inawonongekeratu. Madzi osefukirawo anawononganso Nyumba za Ufumu 11 ndiponso Nyumba ya Msonkhano imodzi.

Makomiti 4 othandiza pa ngozi zadzidzidzi anapangidwa kuti athandize abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi, powatonthoza komanso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Malemba. Komanso anawapatsa zinthu zomwe zinkafunikira mwansanga monga chakudya, zovala komanso madzi abwino. Makomitiwa adzatsogolera ntchito yothandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi yomwe itenga nthawi ndipo idzaphatikizapo kuyeretsa, kupha tizilombo toyambitsa matenda, ndiponso kukonza nyumba za abale athu zomwe zinaonongeka.

Tikupempherera abale ndi alongo athu ku Japan omwe anakhudzidwa ndi madzi osefukirawo pamene tikuyembekezera nthawi imene Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake kuthetseratu masoka onse padzikoli.—Mateyu 8:26, 27.

 

Onani Zambiri