Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 22, 2018
KAZAKHSTAN

Akupempha Kuti Boma la Kazakhstan Limasule Teymur Akhmedov

Akupempha Kuti Boma la Kazakhstan Limasule Teymur Akhmedov

Achibale komanso anzawo a a Teymur Akhmedov ayamba kuwadera nkhawa kwambiri. Zili choncho chifukwa a Akhmedov, omwe ndi a Mboni za Yehova, ali ndi zaka 61 ndipo akhala m’ndende kupitirira chaka chimodzi. Pamene ankamangidwa anali atayamba kale kudwala. Pa 8 February 2018, anachitidwa opaleshoni kuti achotse zotupa ziwiri ndipo chimodzi chinali cha khansa. Achibale komanso maloya awo apempha kuti akuluakulu a boma amasule a Akhmedov m’ndende ya ku Pavlodar chifukwa choti zinthu sizili bwino m’ndendeyo ndipo iwo akufunikira thandizo la kuchipatala. Koma mpaka pano akuluakuluwo anyalanyaza zimene apemphedwazo.

Makhoti a ku Kazakhstan anagamula kuti a Teymur Akhmedov akhale m’ndende kwa zaka 5 moti adzatuluka mu 2022. A Akhmedov ankangogwiritsa ntchito ufulu wawo wa chipembedzo koma anamangidwa n’kuimbidwa mlandu ndi akuluakulu a boma. Akuluakuluwo aika dzina lawo m’gulu la anthu amene sangagwiritse ntchito maakaunti awo a kubanki chifukwa choti akuwakayikira kuti amagwirizana ndi zigawenga. Makhoti a ku Kazakhstan akana kumva maapilo onse.

Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka linapempha boma la Kazakhstan kuti limasule a Akhmedov n’kuvomereza kuti ndi osalakwa. Komanso Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapempha kuti awamasule mwamsanga chifukwa choti akudwala.

Loya wa a Akhmedov anati: “A Akhmedov anamangidwa mopanda chilungamo, akudwala ndipo akufunika thandizo la kuchipatala. Choncho ayenera kumasulidwa kuti chilungamo chichitike. Mofanana ndi magulu a UN, nafenso tikupempha kuti boma la Kazakhstan lichitire chifundo a Akhmedov n’kuwamasula m’ndende mwamsanga.”