Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 21, 2017
KAZAKHSTAN

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Kazakhstan Lakana Apilo ya a Teymur Akhmedov

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Kazakhstan Lakana Apilo ya a Teymur Akhmedov

Pa 4 December 2017 Khoti Lalikulu Kwambiri ku Kazakhstan linakana apilo ya a Teymur Akhmedov yokhudza mlandu wawo womwe akuwaganizira kuti anaphwanya malamulo a boma pochita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo. Koma chilungamo chake n’chakuti a Akhmedov ankangokambirana ndi anthu zomwe iwowo amakhulupirira. Iwo akhala akusungidwa ndi apolisi kuchokera pa 18 January 2017 pomwe apolisi ochita zinthu mwachinsinsi anawamanga mosatsatira malamulo. M’mwezi wa May, khoti la m’dera lawo linawapeza kuti ndi wolakwa ndipo linawagamula kuti akhale m’ndende kwa zaka 5. Mu June 2017, khoti loona za ma apilo linagwirizananso ndi chigamulochi.

Poweruza nkhaniyi, Khoti Lalikulu Kwambiri linanyalanyaza zomwe Gulu la Bungwe la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka linanena. Gululi linapeza kuti dziko la Kazakhstan linalakwitsa pomanga komanso kusunga mokakamiza a Akhmedov popanda zifukwa zomveka. Linapezanso kuti dzikolo linawaphwanyira ufulu wachipembedzo. Ngakhale kuti a Akhmedov akumadwaladwala, akuyesetsabe kulimbitsa chikhulupiriro chawo komanso akudalirabe Mulungu. Iwo akuthokoza kwambiri anthu onse omwe akhala akuyesayesa kupeza njira zowathandizira kuti atuluke m’ndende ngakhale kuti sizinaphule kanthu. Akuthokozanso kwambiri a Mboni anzawo padziko lonse chifukwa choti akupitirizabe kuwapempherera kuti atuluke m’ndende.