Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 6, 2018
KAZAKHSTAN

Anakhala M’ndende Masiku 441—Kucheza Ndi a Teymur Komanso a Mafiza Akhmedov

Anakhala M’ndende Masiku 441—Kucheza Ndi a Teymur Komanso a Mafiza Akhmedov

Pulezidenti wa dziko la Kazakhstan, a Nursultan Nazarbayev, anakhululukira M’bale Teymur Akhmedov ndipo anatulutsidwa m’ndende pa 4 April, 2018. Bambo Akhmedov anakhala m’ndende masiku 441. Iwo anamangidwa chifukwa chouzako ena zimene amakhulupirira.

A Teymur atangotulutsidwa kumene m’ndende, abale a mu ofesi yofalitsa nkhani (Office of Public Information, OPI) ku likulu la Mboni za Yehova ku Warwick, New York, anacheza ndi a Teymur komanso akazi awo a Mafiza omwe panopa anabwerera kunyumba kwawo mu mzinda wa Astana lomwe ndi likulu la dziko la Kazakhstan. M’nkhaniyi muli zimene anafotokoza pamene ankacheza nawo ndipo zinthu zina zasinthidwa pofuna kufupikitsa nkhaniyi komanso kuti imveke bwino.

OPI: Choyamba timafuna kudziwa zambiri zokhudza inuyo M’bale Akhmedov. Kodi munakhala liti wa Mboni za Yehova?

Teymur Akhmedov: Ndinabatizidwa pa 9 October, 2005. Ndisanaphunzire choonadi, sindinkakhulupirira kuti kuli Mulungu. Kwa zaka zambiri sindinkakhulupirira mulungu aliyense kapena chipembedzo chilichonse. Koma kenako mkazi wanga atayamba kuphunzira ndi a Mboni, ndinayamba kuchita chidwi ndi zimene ankaphunzirazo. Ndinkaima kuseli kwa chitseko n’kumamvetsera mobisa zimene ankakambiranazo.

Nditadziwa nkhani zimene ankakambirana, ndinachita chidwi chifukwa ankangonena zinthu zabwino. Kenako, a Mboniwo anakonza zoti ndikumane ndi M’bale Veslav yemwe kwawo kunali ku Poland koma pa nthawiyo ankatumikira ku Kazakhstan. Pa tsiku loyamba limene ndinacheza ndi m’baleyu ndinamuuza kuti: ‘Ndikufunsani funso limodzi lokha. Ngati ndingakhutitsidwe ndi zimene mundiyankhe, mukhala mnzanga ndiponso tipitiriza kucheza. Koma ngati sindigwirizana ndi zimene muyankhe, musadandaule nazo koma sindidzapitiriza kucheza nanu.’ Kenako ndinafunsa M’bale Veslav zimene zimachitika munthu akamwalira. Anatsegula Baibulo pa Mlaliki 9:5 n’kunena kuti, ‘Werengani vesili ndipo mudziwa zimene zimachitika.’ Nditawerenga vesilo ndinazindikira kuti ndapeza choonadi. Ndinavomera kuti tidzakumananso kuti ndidzaphunzirenso Baibulo.

Chabwino, munapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo kenako munabatizidwa mu 2005.

Tsopano tiyeni tikambirane zimene zinachitika musanamangidwe. Mu May 2016, munakumana ndi gulu la azibambo amene ananena kuti ali ndi chidwi ndi zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira. Kwa miyezi ingapo, munaphunzira Baibulo ndi azibambowo kwa nthawi zingapo. Mukaganizira mmene munkachezera ndi azibambowo, kodi panali chilichonse chimene anayankhula kapena kuchita chomwe chinali chokayikitsa?

TA: Inde. Ndinawauza kuti nthawi zambiri timaphunzira Baibulo ndi munthu aliyense payekha osati monga gulu. Ndinawauzanso kuti zingakhale bwino aliyense nditamaphunzira naye payekha. Koma ndikanena zimenezi, iwo ankakana ndipo ankanena kuti amasangalala akamaphunzira monga gulu. Komanso nthawi zambiri ankaitana anzawo ena kuti adzakhale nafe tikamaphunzira, ndipo ankandiuza kuti ndibwereze zimene tinakambirana ulendo watha.

Mafiza Akhmedov: Tsiku lina ndinakhala nawo pamene azibambowo ankaphunzira Baibulo. Ndinazindikira kuti ankakambirana nkhani za zipembedzo zosiyanasiyana ngakhale kuti pofika pa nthawiyi, n’kuti ataphunzira Baibulo kwa nthawi yaitali ndithu. Ndinazindikiranso kuti nyumba imene ankakhala inali yapamwamba kwambiri kusiyana ndi zimene ankakhala ena amene ankaphunziranso Baibulo. Ndinawauzanso kuti anali ndi zinthu zambiri zodula kusiyana ndi anthu ambiri amene ankaphunziranso Baibulo. Zimene ndinanenazi zinawapangitsa kuti asakhalenso omasuka. Pamene ankapita, anatengera a Akhmedov pambali n’kuwauza kuti ineyo ndisadzakhale nawonso pa nthawi yophunzirayo. Pa nthawiyi n’kuti ndikudikirira panja.

Ndi liti pamene munazindikira kuti azibambo amene munkaphunzira nawowo analibe chidwi ndi Mboni za Yehova koma kuti anali apolisi ofufuza zinthu mwachinsinsi?

TA: Ndinazindikira kuti anali apolisi pa nthawi yozenga mlandu ku khoti.

Ndiyeno munachita chiyani atakugwirani kenako n’kukupezani ndi mlandu “woyambitsa chisokonezo pankhani za chipembedzo” komanso “kuchititsa anthu kuganiza kuti chipembedzo chanu n’chapamwamba”?

TA: Kunena zoona, atandigwira, ndinkaganiza kuti apita nane ku polisi kuti ndikafotokoze mbali yanga ngati mmene anandiuzira ndipo kenako andimasula. Ndinali wokonzeka kukadziteteza komanso kufotokoza zimene ndinakambirana ndi azibambowo.

Ndinadabwa kwambiri ndi zimene zinachitika pambuyo pake, koma sindinkaopa. Zimene ankandineneza zoti ndinachititsa anthu kuti azidana ndi anthu azipembedzo zina komanso kuchita zinthu zoopsa, zinandidabwitsa kwambiri. A Mboni za Yehova ndi anthu amene amauza ena za Yehova komanso sanayambe achitapo zinthu zoyambitsa chidani kapena zosokoneza mgwirizano. Ndinadziuza kuti sindinalakwe chilichonse komanso kuti Yehova andithandiza. Ndi zoona kuti ndinkadandaula, koma ndinakumbukira malangizo opezeka m’Baibulo oti ‘muzimutulira [Yehova] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

Kenako, pa 2 May, 2017, mutakhala m’ndende miyezi yoposa itatu popanda kuzenga mlandu wanu, khoti laling’ono ku Astana linagamula kuti mukhale m’ndende za 5 komanso linaonjezera zaka zitatu kuti musamachite chilichonse chokhudza kuphunzira Baibulo. Kodi chigamulo chimenechi chinakukhudzani bwanji?

TA: Khoti litalengeza chigamulo chake, ndinangovomereza kuti ndigwira ukaidi kwa zaka 5. Maganizo anga anali oti: ‘Ngati chimenechi n’chiyeso, ndiye kuti Yehova akudziwa kuti chiyesochi chikhala chachitali bwanji komanso pamene chidzathe.’ Ndinali wokonzeka kudikirira mpaka pamene chiyesochi chidzathere.

Ndende imene M’bale Akhmedov anaikidwamo mu mzinda wa Pavlodar ku Kazakhstan.

Tamva zoti pa nthawi yomwe munkaikidwa m’ndende, munali mukuvutika ndi matenda aakulu. Kodi zimenezi n’zoona?

TA: Inde. Ndisanaikidwe m’ndende, ndimadwala ndipo ndinali kulandira thandizo lamankhwala. Nditamangidwa, ndinasiya kulandira thandizo ndipo matenda anga anayamba kukula.

A Mafiza, kodi munamva bwanji zimenezi zitachitika?

MA: Ndinachita mantha kwambiri komanso ndinada nkhawa kwambiri. Mwamuna wanga atamangidwa, zinali zovuta kwambiri kuti ndipange zosankha pandekha chifukwa pa zaka 38 zimene takhala m’banja, sitinapatukanepo ngati mmene zinalili a Akhmedov atamangidwa. Koma mwamuna wanga anandilimbikitsa ndipo anandiuza kuti: ‘Usadandaule! Ngakhale titasiyana kwa zaka 5 zimenezi, Yehova atidalitsa kwambiri ngakhale tili m’dziko lovutali.’

N’chiyaninso chimene chinakuthandizani pa nthawi imene mwamuna wanu anali m’ndende?

MA: Abale ndi alongo anandithandiza kwambiri. Amuna anga atamangidwa, ndinkaganiza kuti aliyense azichita mantha kudzandiona, ndikaganizira zimene zinachitika pa nthawi imene amuna anga ankamangidwa. Apolisi ankachita zinthu zosonyeza kuti ali ndi chidwi ndi nyumba yathu komanso zomwe tinkachita.

Ndiyeno tsiku lina, mkulu wina ndi mkazi wake anabwera kudzandiona, ndipo zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri. Ndinawafunsa kuti, ‘Simukuchita mantha kuti mwabwera kuno?’ Iwo anandiyankha kuti, ‘Tichite mantha chifukwa chiyani? Masiku ano apolisi akhoza kudziwa zimene tikuchita pogwiritsa ntchito mafoni athu. Ndiye ngati akufuna kutipeza, sangavutike kuchita zimenezi.’

Akulu atabwera kudzachita ulendo waubusa, anandilimbikitsa kuti zimene zinachitikazo zisafooketse chikhulupiriro changa komanso kuti ndilimbitse ubwenzi wanga ndi Yehova.

A Teymur, n’chiyani chinakuthandizani kuti mupirire chiyeso chimenechi komanso kuti muzionabe zinthu moyenera?

M’bale Akhmedov atamangiriridwa ndi maunyolo ku bedi la kuchipatala mu mzinda wa Almaty atangotsala pang’ono kutulutsidwa m’ndende. Ngakhale kuti poyamba sankapatsidwa chithandizo cha mankhwala, akuluakulu a boma anavomera kuti athandizidwe pamene thanzi lawo silinali bwino kwenikweni.

TA: Kupemphera kwa Yehova. Tsiku lililonse ndinkapemphera kuti Yehova anditsogolere, andithandize kumvetsa mmene zinthu zinalili, komanso kuti andipatse mphamvu n’cholinga choti ndikhalebe osangalala, ndikhalebe ku mbali yake, komanso wokhulupirika pa nthawi yovutayi. Ndinkachita kuoneratu kuti Yehova akundiyankha mapemphero anga. Ankandithandiza, ndipo sindinkaona kuti ndinali ndekha m’ndendemo.

Kuwerenga Baibulo kunandithandizanso. Mu ndende ina imene ndinaikidwamo, ndinali ndi mwayi wokhala ndi Baibulo nthawi zonse. M’ndende inanso imene ndinasungidwamo munali laibulale, ndipo mu laibulaleyo munali Baibulo moti ndinkapita kukaliwerenga kamodzi pamlungu.

Ndinkakumbukiranso zimene m’bale amene ankandiphunzitsa Baibulo ananena. Ankakonda kunena kuti sitiyenera kuopa mavuto amene timakumana nawo. Ndikukumbukira kuti tsiku lina ndinamufunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani sindiyenera kuopa? Nanga ndingatani ngati vutolo ndi lalikulu komanso loopsa?’ Iye anandiuza kuti Yehova sadzalola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapirire ndipo adzatipatsa mphamvu kuti tithe kulimbana ndi vuto lililonse. (1 Akorinto 10:13) Ndiye pamene ndinali m’ndende, sindinaiwale mfundo ya palembali.

Kodi munamva bwanji mutazindikira kuti abale ndi alongo padziko lonse akudziwa zimene munakumana nazo komanso kuti akukupemphererani?

TA: Ndinamva kuti Yehova akundithandiza chifukwa gululi ndi lake. Zimenezi zinanditsimikizira kuti Yehova sandisiya komanso kuti tsiku lina adzandipulumutsa.

N’zochititsa chidwi kuti kuikidwa m’ndende ndi chinthu chimene ndinkachiopa kwambiri. Ndinkachita mantha kwambiri ndi ndende. Ndinkati ndikawerenga nkhani za abale amene ali m’ndende, ndinkapemphera kuti, ‘Chonde Yehova, sindikufuna kudzakhala m’ndende!’ Koma pa nthawi imodzimodziyo, ndinkalakalaka kwambiri nditakumana ndi akaidi kuti ndiwauze za choonadi. Nditafunsa abale ngati n’zotheka kuti ndizikalalikira kundende, iwo anandiuza kuti pa nthawiyo, tinalibe chilolezo choti tikhoza kumakalalikira m’ndende. Ndiye pamene ndinkapita kundende, ndinali ndi maganizo awiri osiyana. Ndinali ndi mantha ndikaganizira kuti ndikupita ku ndende, koma ndinkaonanso kuti zimene ndinkalakalaka kuti ndikalalikire akaidi zitheka tsopano.

Ndiyeno, kodi munapeza mpata wolalikira kwa akaidi ena muli m’ndendemo?

TA: Eya. Pa nthawi ina, ndinaitanidwa kuti ndikumane ndi wapolisi wina amene ankafuna kulankhula nane. Nditalowa mu ofesi yake, anandiuza kuti, ‘Ndikudziwa kuti ndiwe wa Mboni za Yehova, ndiye sindikufuna kuti undilalikire.’ Ndiyeno ndinamuyankha kuti, ‘Sikuti ndikufuna kukulalikirani.’ Kenako anandifuna kuti, ‘Kodi dzina la Mulungu ndi ndani?’ Ndinamuuza kuti, ‘Dzina la Mulungu ndi Yehova.’ Anandifunsanso kuti, ‘Ndiye Yesu ndi ndani? Si Mulungu?’ Ndinanena kuti, ‘Ayi, koma ndi mwana wa Mulungu.’ Ndiyeno anandifunsanso kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani Akhristu a Orthodox amakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu?’ Ndinamuyankha kuti, ‘Mukawafunse iwowo zimenezo.’

Pa nthawi ina, ndinali ndi mwayi woyankhula kwa anthu oposera 40 nthawi imodzi. Mayi wina yemwe ndi katswiri wa zamaganizo a anthu anabwera kundendeko kudzaona akaidi. Tinkakambirana nkhani yokhudza banja ndipo iye anatifunsa maganizo athu pa nkhani ya mitala. Aliyense anali ndi mwayi wofotokoza maganizo ake.

Itafika nthawi yoti ndifotokoze maganizo anga, ndinanena kuti ndinalibe maganizo anga pa nkhaniyo, koma ndimasangalala ndi maganizo amene munthu wina ananenapo pa nkhaniyo, omwe ndingakonde kukufotokozerani. Ndiyeno ndinanena kuti munthuyo anati: ‘Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.’ (Genesis 2:24) Ndiyeno mayiyo anandifunsa kuti, ‘Amenewo ndi maganizo a ndani?’ Ndinamuyankha kuti, ‘Amenewa ndi maganizo a Yehova Mulungu, amene analenga anthu onse. Iye anangotchula za anthu awiri basi.’

Ndiyeno mayiyo anandifunsa kuti, ‘Ulinso ndi zifukwa zina zomwe zikukupangitsa kuganiza kuti mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi mmodzi yekha?’ Ndinatchula mfundo ya pa Mateyu 7:12, pomwe pamati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” Ndiyeno ndinati: ‘Mawu amenewa anayankhula ndi Yesu. Ndiye tawafunsani azibambo omwe ali muno ngati angasangalale kuti azigawana mkazi wawo ndi amuna ena. Ngati azibambo safuna kuti mkazi wawo akhalenso ndi mwamuna wina, n’zosachita kufunsa kuti nawonso akazi safuna kuti mwamuna wawo akhale ndi akazi ambirimbiri.’ Kenako mayiyo ananena kuti pa mayankho onse amene anthu anapereka, anakonda kwambiri yankho langa.

N’zosangalatsa kuti ngakhale kuti zinthu sizinali bwino pamoyo wanu, munapeza mwayi wolalikira kwa anthu amene munali nawo.

Makhoti onse, kuphatikizapo Khoti Lalikulu Kwambiri ku Kazakhstan atakana ma apilo amene munapanga kuti mutulutsidwe, zinkaoneka kuti panalibenso kwina komwe mukanapita kuti akuthandizeni.

Komatu munali ndi mwayi wotulutsidwa mukanangosaina chikalata chovomereza kuti zimene munachita zinali zolakwika. Mungatiuze zokhudza mwayi umenewu komanso kuti n’chifukwa chiyani munakana kusaina?

TA: Zoonadi, ndipo anandipatsa mwayi wosainira chikalatacho maulendo angapo. Ngakhale kuti zinkaoneka ngati akundikomera mtima, komatu chikalatacho chinkanena kuti ndinali wolakwa pa mlandu omwe ankandizengawo komanso kuti ndikupepesa chifukwa cha zinthu zomwe ndinachita. Kenako, anandipatsa mwayi woti ndilembe kalata yanga yovomereza kuti zomwe ndinachita zinali zolakwika komanso kuti ndikupempha kuti andikhululukire. Oyang’anira ndende anandiuza kuti ndilembe kalata yonena kuti ndinalakwitsa pouza anthu ena zimene ndimakhulupirira ndipo kuti ndikupepesa chifukwa cha zimene ndinachita, komanso kuti ndikupempha kuti anditulutse chifukwa ndinali kudwala.

Ndinakana kuvomera zonsezo ndipo ndinauza oyang’anira ndendewo kuti bola ndikhale m’ndende koma ndili ndi chikumbumtima choyera, kusiyana n’kuti nditulutsidwe chikumbumtima changa chikundivutitsa.

Tikuyamikira kwambiri chitsanzo chanu posonyeza chikhulupiriro komanso pokana kuchita zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chanu.

Koma kenako, zinthu zinasintha mosayembekezereka. Tiuzeni kuti munadziwa bwanji kuti mukhululukidwa n’kutulutsidwa m’ndende?

TA: Tsiku lina mlonda wina anabwera m’chipinda chomwe ndinaikidwa kudzandiuza kuti ndikayankhe foni. Ndikukumbukira kuti m’maganizo mwanga ndinadzifunsa kuti: ‘Ndani angandiimbire?’ Nditayankha foniyo, mzimayi wina anandiuza dzina lake n’kunena kuti akubwera kudzanditulutsa m’ndendemo. Sindinadziwe zoti ndinene nditamva zimene ndinauzidwa pafoniyo. Ndiyeno atadula foniyo, ndinaganiza zomuuza mwana wanga wamwamuna nkhaniyi chifukwa sindinkafuna kumudzidzimutsa mkazi wanga akamva nkhaniyi, kapena kumupatsa chiyembekezo choti nditulutsidwa ndisanatsimikizire.

Nditamaliza kulankhula pafonipo mlonda uja anandifunsa kuti: ‘Amakuuzani zotani pafonipo?’ Ndinamuuza kuti winawake akufuna kungondiputsitsa chifukwa mzimayiyo anangonena kuti akubwera kudzanditulutsa m’ndendemo.

A Mark Sanderson a m’Bungwe Lolamulira limodzi ndi a Teymur komanso a Mafiza Akhmedov, pambuyo poti M’bale Akhmedov wangotulutsidwa kumene m’ndende.

Mlondayo anandiuza kuti mzimayiyo samanama ndipo kuti zimene amanenazo zinali zoona.

A Mafiza, kodi munatani mutamva nkhani yosangalatsa kwambiri imeneyi?

MA: Mwana wanga atandiuza za nkhaniyi, nanenso ndinkangoona ngati ndi zonama. Tinakhala tikudikirira kumva nkhani imeneyi kwa nthawi yaitali.

Tikuganizadi kuti zinali zosangalatsa kwambiri mutakumananso pambuyo pa chaka choposa chimodzi a Teymur atamangidwa.

Ndiyeno mukaganizira zomwe zinakuchitikiranizi, kodi mwaphunzira zotani mukaona mmene zimenezi zinayesera chikhulupiriro chanu?

MA: Ndikukumbukira kuti ndinkalira ndikaganizira zomwe zinachitikira M’bale Bahram [Hemdemov] komanso Mlongo Gulzira Hemdemov. [M’bale Hemdemov anamangidwa mu March 2015 ndi akuluakulu a boma m’dziko la Turkmenistan. Pa 19 May, 2015, anagamulidwa kuti akhale m’ndende powanamizira kuti “ankalimbikitsa anthu kudana ndi anthu azipembedzo zina” ndipo panopa akadali m’ndende.] Ngakhale pamene a Teymur anali asanamangidwe, ndinkaganizira mmene Gulzira zinam’khudzira a Bahram atamangidwa. Ndiye panopa ndikufuna kumukumbatira ndi kumuthandiza komanso kuti adziwe kuti ndimamukonda kwambiri. Popeza a Teymur nawonso anakumana ndi vuto lomweli, ndikufuna kumuuza kuti ndikumvetsa mmene zimenezi zikum’pwetekera. Ndikudziwa kuti nayenso ayenera kudalira Yehova komanso abale kuti amuthandiza ngati mmene athandizira ineyo.

Ndikuthokoza kwambiri abale ndi alongo onse amene anatithandiza, a mumpingo wathu komanso m’mipingo yonse padziko lonse, Bungwe Lolamulira, maloya, ndiponso ana athu.

M’bale Akhmedov pambuyo poti atulutsidwa m’ndende. Anyamula satifiketi yosonyeza kuti akhululukidwa.

TA: Ndikungofuna kunena chinthu chimodzi chokha. Pali mayesero amene aliyense ayenera kukumana nawo. N’zoona kuti si kuti aliyense adzakumana ndi chiyeso chomangidwa n’kuikidwa m’ndende. Ena angayesedwe pozunzidwa ndi anthu a m’banja lawo omwe si Mboni. Pomwe ena, mwina akuvutika kuchita zinthu ndi m’bale kapena mlongo mumpingo chifukwa choti ndi wovuta kuchita naye zinthu. Kaya tikukumana ndi mayesero kapena mavuto otani, aliyense ali ndi ufulu wosankha kugwiritsa ntchito mfundo za Mulungu kapena kuzinyalanyaza. Ngati titatsatira mfundo za Mulungu, tingapambane mayeserowo bwinobwino. Chofunika kwambiri kuchita ndi kuvomereza mayeserowo komanso tizikumbukira kuti Yehova adzatipatsa mphamvu kuti tipirire kapena kuthana ndi mayeserowo.

Ndikuyamikira kwambiri banja langa komanso ana anga pondithandiza. Iwo ankagwiritsa ntchito mpata uliwonse kubwera kudzandiona ndipo zimenezi zinandithandiza kukhalabe olimba.

Komanso ndikufuna kuthokoza gulu lonse la abale padziko lonse chifukwa cha zonse zimene anandichitira. Ndinayamikira mapemphero awo komanso makalata awo olimbikitsa. Sindinkamva kuti ndili ndekha ngakhale pang’ono. Zimene zandichitikirazi zandichititsa kuti ndiwonjezere chikondi changa ku gulu lonse la abale komanso zalimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova.