APRIL 18, 2018
KAZAKHSTAN
A Teymur Akhmedov Anakhululukidwa ndi Pulezidenti Ndipo Anatulutsidwa M’ndende
Pa 2 April, 2018, Pulezidenti Nursultan Nazarbayev wadziko la Kazakhstan anakhululukira a Teymur Akhmedov omwe ali ndi zaka 61 atakhala m’ndende kwa chaka ndi miyezi pa mlandu wongowanamizira. Zimenezi zachititsa kuti asakhalenso ndi mbiri yoti anapalamulapo mlandu m’dzikolo. A Akhmedov anauzidwa kuti atulutsidwa m’ndende pa 4 April ndipo panthawiyi n’kuti akadali m’chipatala pambuyo popangidwa opaleshoni. Panopa ali limodzi ndi banja lawo ndipo azilandira mosavuta thandizo la mankhwala a matenda a khansa.
Anagwidwa, Kusungidwa Komanso Kutsekeredwa M’ndende Wosalakwa
A Akhmedov ndi a Mboni za Yehova ndipo anamangidwa n’kutsekeredwa m’ndende pa 18 January, 2017 chifukwa chouzako ena zimene amakhulupirira. Miyezi ingapo asanamangidwe, anakambirana mfundo za m’Baibulo ndi azibambo ena omwe ankanamizira ngati amafuna kudziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira. Azibambowo anali atagwirizana ndi a polisi ofufuza zinthu mwachinsinsi (National Security Committee) a m’dzikolo ndipo ankajambula mobisa zomwe ankakambiranazo. Apolisiwo anagwiritsa ntchito zomwe azibambowo anajambula poimba mlandu a Akhmedov “woyambitsa chisokonezo pa nkhani ya chipembedzo” komanso “kuchititsa anthu kuganiza kuti chipembedzo chawo n’chapamwamba,” zomwe n’zosemphana ndi Gawo 174 ndime 2 la m’buku la malamulo a zaupandu a dziko la Kazakhstan.
A Akhmedov atamangidwa, apolisi anawafunsa mafunso kenako anawatsekera m’ndende kwa miyezi itatu asanawazenge mlandu. Pa 2 May, 2017, a Khoti anagamula kuti akhale m’ndende kwa zaka 5 ndipo anawaletsanso kuchita zinthu zokhudza chipembedzo chawo kwa zaka zitatu zowonjezera.
Makhoti anakana kuti a Akhmedov atulutsidwe ngakhale kuti maloya awo anachita apilo kambirimbiri za nkhaniyi. A Akhmedov anayesa njira zonse kuti makhoti a ku Kazakhstan awathandize koma zinakanika, ndipo anakatula nkhaniyi ku makhoti a mayiko ena. Iwo anakadandaula za nkhaniyi ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka komanso ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu.
Mu October 2017, Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka linanena kuti boma la Kazakhstan linalakwitsa kumanga a Akhmedov. Gululi linalamula kuti boma la Kazakhstan litulutse bambowa mwamsanga chifukwa zomwe a Akhmedov anachita “zinali zosayambitsa chisokonezo ngakhale pang’ono komanso sanagwiritse ntchito ufulu wawo wachipembedzo mopitirira malire.” Mu January 2018, Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inamva dandaulo la a Akhmedov ndipo inalamula boma la Kazakhstan kuti lionetsetse kuti bambowa akulandira thandizo la mankhwala lokwanira. Komitiyi inauzanso boma la Kazakhstan kuti liganizirenso zotulutsiratu m’ndende bambo Akhmedov pa nthawi imene akudikira chigamulo pa dandaulo lawo.
Anatulutsidwadi
Pa nthawi imene a Akhmedov anali m’ndende ankangodwaladwala ndipo thanzi lawo silinali bwino. Kumayambiriro kwa chaka chino, madokotala anauza bambo Akhmedov kuti ali ndi khansa ya m’matumbo yomwe yafalikira kwambiri. Chifukwa cha zimene Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu komanso mabungwe a m’mayiko ena ananena pa nkhaniyi, akuluakulu a boma la Kazakhstan anauza bambo Akhmedov kuti alembere Pulezidenti Nazarbayev kalata yopempha kuti awakhululukire.
Iwo analemba kalatayo pa 5 March, 2018 ndipo anapempha kuti awayankhe mwamsanga chifukwa akufunika kulandira mwachangu mankhwala omwe angathandize kuti khansa isiye kufalikira. Pa nthawiyi akuluakulu a ndende anasamutsira a Akhmedov ku Almaty, komwe anakachitidwa opaleshoni pa 27 March, 2018.
Kodi Boma la Kazakhstan Liyamba Kulemekeza Kwambiri Ufulu Wopembedza?
Panopa bambo Akhmedov, akazi awo a Mafiza komanso ana awo ndi osangalala kwambiri kuti mavuto amene ankakumana nawo atha. Akuyamikiranso kwambiri kuti Pulezidenti wa dzikolo a Nazarbayev anathandiza kuti asakhalenso ndi mbiri yoti anapalamulapo mlandu m’dzikolo. Bambo Akhmedov atamangidwa mopanda chilungamo, boma la Kazakhstan linatseka akaunti yawo ya ku banki ndipo zimenezi zinachititsa kuti akazi awo ndi ana avutike kwambiri pamene iwo anali m’ndende.
A Mboni za Yehova padziko lonse akukhulupirira kuti kukhululukidwa kwa bambo Akhmedov kuthandiza kuti panopa akuluakulu a boma la Kazakhstan avomereze kuti a Mboni za Yehova azipatsidwa ufulu wolambira mwamtendere popanda vuto lililonse.