SEPTEMBER 4, 2019
KENYA
A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chiluo ku Kenya
Pa 30 August, 2019, a Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la chinenero cha Chiluo pamsonkhano wachigawo womwe unachitikira mumzinda wa Kisumu ku Kenya. M’bale Remy Pringle wa m’Komiti ya Nthambi ku Kenya, anatulutsa Baibuloli pa tsiku loyamba la msonkhanowu. Anthu 2,481 kuphatikizapo ena omwe anaonera msonkhanowu kuchokera kumalo ena awiri, ndi amene anapezeka pamsonkhanowu.
Ntchito yomasulira Baibuloli inatenga zaka pafupifupi zitatu. Mmodzi mwa anthu omwe anagwira nawo ntchito yomasulira Baibuloli anati: “Baibuloli lithandiza kwambiri abale ndi alongo omwe ankafunitsitsa kukhala ndi Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu la Chiluo. Mabanja ambiri m’mipingo yathu sakanakwanitsa kugula Baibulo lathunthu kuti aliyense m’banjamo akhale nalo, choncho likhala dalitso aliyense akakhala nalo lake. Komanso Baibuloli lalembedwa m’chinenero chamakono chomwe ndi chosavuta kumva ndipo zimenezi zithandiza kulimbitsa kwambiri chikhulupiriro munthu akamaligwiritsa ntchito pophunzira payekha komanso pa kulambira kwa pabanja.”
Baibulo la Dziko Latsopano lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’zinenero 184, kuphatikizapo Mabaibulo a zinenero 25 omwe akonzedwanso mogwirizana ndi la Chingelezi lomwe linatulutsidwa mu 2013. Tikukhulupirira kuti Baibuloli lithandiza ofalitsa pafupifupi 1,800 olankhula Chiluo omwe ali m’gawo la nthambi ya Kenya kuti apitirize kuyandikira kwa Yehova. Lithandizanso pa ntchito yolalikira mogwira mtima kwa anthu oposa 5 miliyoni omwe amalankhula Chiluo.—Mateyu 24:14.