NOVEMBER 19, 2019
KENYA
Nyumba Yatsopano ya Masukulu Ophunzitsa Baibulo Aitsegulira ku Kenya
Nyumba yatsopano ya masukulu ophunzitsa Baibulo anaitsegulira pa 9 November, 2019, mumzinda wa Eldoret ku Kenya. M’bale Bengt Olsson wa m’Komiti ya Nthambi ya Kenya ndi amene anakamba nkhani yotsegulira nyumbayi ndipo anthu 1,199 anamvetsera nkhaniyi kuphatikizapo anthu 500 a muutumiki wanthawi zonse wapadera ochokera m’madera osiyanasiyana m’dzikolo. Nyumbayi ndi yaikulu mamita 433 m’mbali zake zonse ndipo muzidzachitikira Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu komanso Sukulu ya Oyang’anira Madera ndi Akazi Awo. Pa chaka, makalasi osachepera 4 a Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu azichitikira m’nyumbayi.
Pamalo omwe pali sukuluyi palinso nyumba zosiyanasiyana za ofesi ya nthambi zomwe zinakonzedwa. Nyumba yomwe kale inali ya amishonale yakonzedwanso kuti ikhale ndi malo ochapira zovala, khitchini, komanso chipinda chodyera. Nyumba ya Ufumu inasinthidwa kuti ikhale kalasi. Ntchitoyi inayamba pa 1 April, 2019, ndipo mbali yaikulu inamalizidwa pa 9 September.
Ponena za kufunika kwa sukuluyi, M’bale Olsson anati: “Pali anthu ambiri omwe ndi okonzeka kuphunzira za Yehova Mulungu ku East Africa. Sitikukayikira kuti maphunziro omwe ophunzira azilandira athandiza kuti m’tsogolomu ntchito yophunzitsa anthu Baibulo ipitirize kuwonjezeka pamene anthu akukhamukira ku phiri la Yehova.”—Mika 4:1.