Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Hotelo ya ku Dusit mumzinda wa Nairobi ku Kenya, komwe zauchigawengazi zinachitikira.

JANUARY 25, 2019
KENYA

Zigawenga Zapha Anthu Pamalo Amene Pali Hotelo Ina ku Kenya

Zigawenga Zapha Anthu Pamalo Amene Pali Hotelo Ina ku Kenya

Pa 15 January, 2019, anthu osachepera 21 anaphedwa ndi zigawenga zina pamalo omwe pali hotelo komanso maofesi mumzinda wa Nairobi ku Kenya.

Ofesi ya nthambi ku Kenya yanena kuti palibe wofalitsa aliyense amene anaphedwa kapena kuvulazidwa chifukwa cha zauchigawengazo, zomwe zinachitikira pamtunda wa makilomita 7 kuchokera komwe kuli ofesi ya nthambi. Abale ndi alongo oposa 10 amagwira ntchito pamalo omwe panachitika zauchigawengazi, ndipo malowo amadziwika kuti Dusit. Pa tsiku lomwe zauchigawengazo zinachitika, a Mboni 7 sanapite ku ntchito ndipo enawo anapulumutsidwa. Pa a Mboni omwe anapulumutsidwa panali m’bale ndi mlongo omwe anabisala kwa maola 12 pa nthawi yomwe zigawengazo zinafika pamalowa.

Akulu komanso oyang’anira madera akuthandiza ofalitsa omwe anakhudzidwa powalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo. Tikupemphera kuti Yehova apitirize kutonthoza abale athuwa pa nthawi yovutayi.—2 Akorinto 1:3, 4.