Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 2, 2015
KYRGYZSTAN

Akuluakulu a Boma ku Kyrgyzstan Sakumanga Mfundo Imodzi pa Nkhani ya Ufulu Wachipembedzo

Akuluakulu a Boma ku Kyrgyzstan Sakumanga Mfundo Imodzi pa Nkhani ya Ufulu Wachipembedzo

Pa September 4, 2014, Komiti ya Khoti Lalikulu Yoona za Malamulo ku Kyrgyzstan inanena kuti, malamulo ena okhudza zipembedzo amene anakhazikitsidwa mu 2008 si ogwirizana ndi malamulo a dzikolo. Izi zinakhudza ufulu wachipembedzo m’dzikoli. Zimenezi zinachititsa kuti a Mboni za Yehova akhale ndi mwayi wokalembetsa chipembedzo chawo m’zigawo za kumwera kwa dzikoli. a

Komabe, komiti ina yoona za zipembedzo m’dzikolo (State Committee on Religious Affairs), ikukanabe kuti a Mboni akalembetse chipembedzo chawo m’zigawo za kumwera kwa Kyrgyzstan. Komitiyi ikunena kuti malamulo okhudza zipembedzo sangasinthe pokhapokha nyumba yamalamulo itakonza malamulo omwe anakhazikitsidwa mu 2008. Izi zikuchititsa kuti a Mboni avutike kukalembetsa chipembedzo chawo. Ndipotu n’zodabwitsa kuti a Mboni Yehova m’zigawo za kumpoto kwa dzikoli akugwira ntchito yawo mwamtendere pamene m’zigawo za kumwera ntchito yomweyo ndi yoletsedwa. b

Anamangidwa Chifukwa Chogwira Ntchito Yolalikira Mosavomerezedwa ndi Boma

Pa June 30, 2014, mu mzinda wa Naryn m’dzikolo, mayi wina wa zaka 46 dzina lake Zhyldyz Zhumalieva ankalalikira zimene amakhulupirira kwa anthu a m’dera lawo. Kenako akuluakulu a boma anamanga mayiyu pa mlandu wofalitsa zimene amakhulupirira monga membala wachipembedzo choletsedwa m’deralo. c Aka n’koyamba kuti wa Mboni amangidwe chifukwa chogwira ntchito yolalikira kuchokera pamene dziko la Kyrgyzstan linalandira ufulu wodzilamulira.

Pa August 5, 2014, khoti la m’boma la Naryn linayamba kuzenga mlandu wa apilo wokhudza mayi Zhumalieva. Oweruza anafunsa mafunso ambirimbiri pofuna kudziwa zokhudza a Mboni za Yehova ndiponso uthenga umene amalalikira kwa anthu. Atamva bwinobwino zokhudza a Mboni, oweruzawo anaimitsa kaye mlanduwu poyembekezera kuti zimene Komiti ya Khoti Lalikulu Yoona za Malamulo inanena ziyambe kugwira ntchito.

Patapita nthawi, khoti la m’boma la Naryn linayambiranso kuzenga mlandu wa mayi Zhumalieva. Khotili silinapeze mayiwa ndi mlandu uliwonse ndipo linapezanso kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wouza anthu ena zimene amakhulupirira. Ndiyeno khotili litaunikanso zimene Komiti ya Khoti Lalikulu Yoona za Malamulo inanena pa September 4, 2014, linapeza kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chinalembetsedwa kale ku boma. Khotili linathetsa mlanduwu koma woimira boma pa milandu anachita apilo ponena kuti zimene Komiti ya Khoti Lalikulu inanena sizingagwire ntchito pa anthu amene apalamula mlandu. Koma pa December 24, 2014, khoti la apilo linakana zimenezi. Choncho linagwirizana ndi zimene khoti la m’boma la Naryn linagamula zoti mayi Zhumalieva ali ndi ufulu wolalikira kwa anthu ena zokhudza zimene amakhulupirira.

Akuluakulu a Mzinda wa Osh Anachita Zinthu Mwachilungamo pa Milandu Yomwe a Mboni Anangonamiziridwa

Mu 2013, apolisi anauza mtsikana wina dzina lake Oksana Koriakina ndi mayi ake a Nadezhda Sergienko, kuti aikidwa pa ukaidi wosachoka panyumba chifukwa chouza anthu ena zimene amakhulupirira. Akuluakulu a mumzinda wa Osh anagwiritsa ntchito milandu yabodzayi pofuna kusonyeza kuti a Mboni za Yehova akugwira ntchitoyi mozembera malamulo. Iwo ananenanso kuti a Mboni si ololedwa m’pang’ono pomwe kumauza anthu ena zimene amakhulupirira, chifukwa chipembedzo chawo n’chosalembetsedwa ku boma.

Khoti la mumzinda wa Osh, linathetsa mlanduwu ndipo linagamula kuti azimayi awiriwa sanapalamule mlandu uliwonse. Pa October 7, 2014, woweruza anamalizitsa mlanduwu ponena kuti apolisi amene ankafufuza zokhudza mlanduwu analakwitsa kwambiri ndipo anamanga amayiwa chifukwa chakuti anali a Mboni basi.

Koma woimira boma pa mlanduwu ku Osh, ankafunitsitsa kuti amayiwo agamulidwe kuti ndi olakwa. Iye ananena kuti apolisi ofufuza milandu akafufuzenso bwinobwino n’cholinga choti akakonze zina ndi zina zomwe zinalakwika poyamba komanso kuti amayiwa adzalowenso m’khoti. Khoti la apilo linakana zimenezi ndipo woimira boma pa mlanduwu anakachitanso apilo ku khoti lalikulu kwambiri ku Kyrgyzstan ndipo khotilo linakonza zoti mlanduwu udzazengedwenso pa March 3, 2015. Amboni za Yehova akukhulupirira kuti mlanduwu udzagamulidwa mowakomera.

Kodi Boma la Kyrgyzstan Likhazikitsa Lamulo Lotani Lokhudza Ufulu Wachipembedzo?

Wa Mboni wina amene anamvetsera nawo mlandu wa mayi Zhumalieva ananena kuti: “Kuyambira mu 1988, akuluakulu a boma akhala akutivutitsa chifukwa chakuti chipembedzo chathu n’chosalembetsedwa ku boma la Naryn. Koma panopa tikuyembekezera kuti mwina tingalembetse chipembedzo chathu ku boma, potengera zimene khoti lalikululi lanena.”

A Mboni za Yehova akuyembekezera mwachidwi nthawi yomwe adzalembetse chipembedzo chawo mumzinda wa Naryn ku Osh komanso m’madera ena a kumwera kwa dzikoli. Izi zidzathandiza kuti azichita zinthu zokhudza chipembedzo chawo mwamtendere. Boma la Kyrgyzstan likatsatira zimene khoti lalikulu lagamula ndiye kuti lilimbikitsa ufulu wachipembedzo wa nzika zake.

a Werengani nkhani yakuti “Khoti Lalikulu ku Kyrgyzstan Lateteza Ufulu Wachipembedzo wa a Mboni za Yehova,” ndipo ikufotokoza zimene Komiti ya Khoti Lalikulu Yoona za Malamulo inanena pa September 4, 2014.

b A Mboni za Yehova analembetsa chipembedzo chawo ku boma ndiponso m’madera ena a kumpoto kwa dzikoli. Koma akuluakulu a boma amakana kuti a Mboni alembetse chipembedzo chawo m’madera a kumwera.

c Gawo 395(2) la malamulo a dziko la Kyrgyzstan limaletsa kuphwanya malamulo ochita misonkhano ya chipembedzo, zionetsero ndiponso miyambo ina ya zipembedzo.