Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 1, 2019
KYRGYZSTAN

Nkhani Yosangalatsa Yokhudza Zamalamulo ku Osh M’dziko la Kyrgyzstan

Nkhani Yosangalatsa Yokhudza Zamalamulo ku Osh M’dziko la Kyrgyzstan

Pa 30 November, 2018, a Unduna wa Zachilungamo ku Kyrgyzstan analemba ofesi ya Mboni za Yehova kukhala yovomerezeka ndi boma mumzinda wa Osh womwe ndi wachiwiri pamizinda ikuluikulu kwambiri ku Kyrgyzstan.

Chipembedzo cha Mboni za Yehova chinalembetsedwa m’dziko la Kyrgyzstan ndipo chakhala chili chovomerezeka ndi boma kungoyambira mu 1998. Koma mu 2008, lamulo latsopano lokhudza zipembedzo litangokhazikitsidwa, akuluakulu a boma akhala akukaniza abale athuwa kulembetsa m’mizinda yomwe ili kum’mwera kwa dzikolo komwenso kuli mzinda wa Osh. Zimenezi zimachititsa kuti akuluakulu a mizinda aziona kuti misonkhano yathu yampingo komanso ntchito yolalikira ndi zosavomerezeka ndi boma. Kwa nthawi zingapo, apolisi akhala akuthyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni komanso malo ochita kupanga lendi omwe abale athu ankasonkhanamo.

Tikusangalala kuti nkhaniyi ithandiza a Mboni ku Kyrgyzstan kuti apatsidwe ufulu wosonkhana momasuka komanso kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa ena mwamtendere.—1 Timoteyo 2:1-4.