Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 14, 2020
LEBANON

Kuphulika kwa Zinthu Zina Kwachititsa Ngozi Yaikulu Mumzinda wa Beirut ku Lebanon

Kuphulika kwa Zinthu Zina Kwachititsa Ngozi Yaikulu Mumzinda wa Beirut ku Lebanon

Pa 4 August 2020, zinthu zina zinaphulika mumzinda wa Beirut, m’dziko la Lebanon ndipo zinachititsa ngozi yaikulu. Malo ena ofikira sitima mumzindawu anasakazidwa koopsa. Anthu ambiri anavulala ndipo nyumba zambiri zinagwetsedwa. Nyumba za abale ndi alongo ena zinawonongedwanso. Mwatsoka, abale ndi alongo ena anavulala kwambiri koma palibe amene anafa.

Sitikukayikira kuti Mulungu wathu wowolowa manja apitiriza kuthandiza atumiki ake pa nthawi yovutayi.—2 Samueli 22:3.