Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 11, 2021
MALAWI

Buku la Mateyu Linatulutsidwa M’Chinenero Chamanja cha ku Malawi

Buku la Mateyu Linatulutsidwa M’Chinenero Chamanja cha ku Malawi

Pa 8 August 2021, M’bale Mark Hutchinson, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku Malawi, anatulutsa buku la m’Baibulo la Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyu m’Chinenero Chamanja cha ku Malawi. Limeneli ndi buku loyamba la m’Baibulo kutulutsidwa m’Chinenero Chamanja cha ku Malawi.

Buku la m’Baibuloli linatulutsidwa pa pulogalamu imene inajambulidwa ndipo inaulutsidwa kumadera onse a ku Malawi. Pulogalamuyi inaulutsidwanso pasiteshoni imodzi ya TV ndi ya wailesi m’dzikoli.

Mpingo woyamba wa m’chinenero chamanja unakhazikitsidwa ku Lilongwe mu 2005. Mu 2009, mabuku anayamba kumasuliridwa m’Chinenero Chamanja cha ku Malawi. Kuyambira nthawi imeneyo, mabuku okwanira 34 amasuliridwa m’chinenero chimenechi. Panopa pali matimu omasulira m’chinenerochi okwana 5 ndipo anthu onse amene amagwira ntchitoyi ndi okwanira 21.

Munthu wina amene anamasulira nawo bukuli, yemwe ali ndi vuto losamva, anati: “Tinkadalira kwambiri malemba osiyanasiyana omwe anamasuliridwa m’chinenero chamanja m’mabuku athu. Koma panopa tili ndi mavesi onse a m’buku la m’Baibuloli omwe angatithandize pophunzira Baibulo patokha komanso mu utumiki.”

Chitsanzo chosonyeza kuti buku la m’Baibuloli linamasuliridwa momveka bwino chili pa Mateyu 22:44. Womasulira wina anafotokoza kuti: “M’Mabaibulo ena vesili limanena kuti ‘Ambuye ananena kwa Ambuye wanga.’ Zimenezi zachititsa anthu ena kukhulupirira kuti Yehova ndi Yesu ndi munthu mmodzi. Koma m’buku la Mateyu limene langotulukali, zikuonekeratu kuti Yehova ndi amene ankalankhula kwa Ambuye Yesu.”

Tikupemphera kuti mphatso imene abale ndi alongo a ku Malawi alandirayi iziwathandiza kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova, yemwe amapereka ‘mphatso iliyonse yangwiro.’​—Yakobo 1:17.