Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ofesi ya nthambi yomwe ili ku Lilongwe, Malawi. Zithunzi zina (kuyambira kumanzere pamwamba): M’bale Bill McLuckie, mtumiki wa nthambi woyambirira ku Malawi; Apolisi akutseka ofesi ya nthambi mu 1967, Mlongo akulalikira mosangalala masiku ano

28 DECEMBER 2023
MALAWI

Patha Zaka 75 Kuchokera Pamene Ofesi ya Nthambi Yoyambirira ku Malawi Inakhazikitsidwa

Mbiri Yokhudza Kupirira Kwawo

Patha Zaka 75 Kuchokera Pamene Ofesi ya Nthambi Yoyambirira ku Malawi Inakhazikitsidwa

Patha zaka 75 kuchokera pamene ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova yoyambirira inakhazikitsidwa ku Malawi, mumzinda wa Blantyre m’chaka cha 1948.

Poyamba, ofesi ya nthambi ya South Africa ndi yomwe inkayendetsa ntchito za Mboni za Yehova ku Malawi. Kungoyambira m’ma 1930, chiwerengero cha abale ndi alongo omwe amatumikira ku Malawi chinakula kwambiri kuchoka pa 28 mu 1934, kufika pa 5,600 mu 1948. Pamene chiwerengero cha a Mboni chinkakula, ofesi yoyamba inatsegulidwa m’nyumba yaing’ono yomwe ankachita lendi ku Blantyre pa 1 September 1948. Ofesiyi inkagwiritsidwabe ntchito mpaka pamene Beteli yatsopano inamangidwa pafupi ndi malowa mu 1958.

Kumanzere: Omasulira zinenero za Chichewa ndi Chitumbuka aima panja pa ofesi ya nthambi yomwe inamangidwa ku Malawi mu 1958. Pali a Baston Nyirenda (mzere wozungulira), omwe panopa akutumikira mu Komiti ya Nthambi ya Malawi. Kumanja: a Nyirenda, azaka 80 ndi akazi awo a Violet, masiku ano

Pasanathe zaka 10, mu October 1967, akuluakulu a boma analetsa ntchito ya Mboni za Yehova ku Malawi. Zitatero, ofesiyi inalandidwa. Komabe, abale omwe ankayang’anira ntchitoyi ku Malawi anapitiriza kutsogolera pa ntchito yolalikira komanso kuthandiza abale ndi alongo m’dzikolo. Kenako kwa zaka pafupifupi 26, a Mboni za Yehova anazunzidwa kwambiri chifukwa chokana kulowerera mu ndale ndipo ankachitiridwa nkhanza zoopsa. Pa nthawi imeneyi, abale ndi alongo athu anamangidwa, kuzunzidwa ndipo ena anaphedwa. Abale ndi alongo ena anasankha kuthawira m’mayiko apafupi monga ku Mozambique, Zambia ndi Zimbabwe.

Abale ndi alongo akumasulira mabuku ofotokoza Baibulo mu Chichewa

Kenako pa 12 August 1993, chipembedzo cha Mboni za Yehova chinatsegulidwanso. Kwa zaka ziwiri, abale a ku Zambia omwe ankatsogolera pa ntchito yolalikira ku Malawi pa nthawi yomwe inali yoletsedwa, anapitiriza kugwira ntchitoyi. Kenako abale anagula nyumba ziwiri mumzinda wa Lilongwe kuti zizigwiritsidwa ntchito ngati ofesi ya nthambi yatsopano. Mu 1994, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti abale apeze malo abwino oti amangepo ofesi ya nthambi yatsopano m’dzikoli. Pa 19 May 2001, abale ndi alongo oposa 2,000 anapezeka pamwambo wopereka ofesi ya nthambiyi kwa Yehova ndipo ambiri mwa abale ndi alongowa anapirira pa nthawi imene ankazunzidwa kwa zaka zambiri. Mmodzi mwa abale amene anapezeka pamwambowu anali M’bale Trophim Nsomba, yemwe anatumikira monga woyang’anira dera pa nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa. Poona mmene ntchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopanoyi inapitira patsogolo ku Malawi, M’bale Nsomba ananena kuti: “Yehova watidalitsa kwambiri ndipo ine ndi mkazi wanga timangomva ngati tikulota.”

Panopa ku Malawi kuli mipingo 1,924 ndipo m’mipingoyi muli abale ndi alongo oposa 109,000. Chiwerengerochi chikuphatikizapo abale ndi alongo 225 omwe akutumikira ku ofesi ya nthambi ya Malawi ku Lilongwe ndipo amagwira ntchito yomasulira mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero 7.

Ena mwa abale ndi alongo 109,000 omwe akutumikira Yehova mokhulupirika ku Malawi masiku ano

Ndi pemphero lathu kuti Yehova apitirize kudalitsa abale ndi alongo athu ku Malawi amene anayesetsa kusonyeza kuti ndi atumiki a Mulungu popirira kwa zaka zambirimbiri.​—2 Akorinto 6:4.